1 Mbiri 17 BL92

Yehova salola Davide ammangire Kacisi

1 Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwace, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma Gkasa la cipangano likhala m'nsaru zocinga.

2 Ndipo Natani anati kwa Davide, Mucite zonse ziri m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu.

3 Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti,

4 Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo;

5 pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku tija ndinakwera naye Israyeli, kufikira lero Gno; koma wa m'hema m'hema Ine, ndi wa m'kacisi m'kacisi,

6 Pali ponse ndinayenda nao Aisrayeli onse ndinanena kodi mau ndi woweruza ali yense wa Israyeli, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?

7 Cifukwa cace tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli;

8 ndipo ndakhala ndi iwe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akuru okhala padziko.

9 Ndipo ndaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;

10 ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israyeli; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

11 Ndipo kudzacitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.

12 Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wace kosatha.

13 Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;

14 koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa cifumu wace udzakhazikika kosatha.

15 Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.

Conena Davide

16 Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?

17 Ndipo ici ncacing'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.

18 Anenenjinso Davide kwa Inu za ulemu wocitikira mtumiki wanu? pakuti mudziwa mtumiki wanu.

19 Yehova, cifukwa ca mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwacita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikuru izi zonse.

20 Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.

21 Ndiwo ayani akunga anthu anu Israyeli, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikuru ndi zoopsa, pakupitikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Aigupto?

22 Pakuti anthu anu Israyeli mudawayesa anthu anu anu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao.

23 Ndipo tsopano, Yehova, akhazikike kosalekeza mau mudanenawa za mtumiki wanu, ndi za nyumba yace, nimucite monga mwanena.

24 Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israyeli; akhalira Israyeli Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu.

25 Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu.

26 Ndipo tsopano, Yehova, Inu ndinu Mulungu, ndipo mwanenera mtumiki wanu cokoma ici;

27 cakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29