1 NDIPO Solomo mwana wa Davide analimbikitsidwa m'ufumu wace, ndipo Yehova Mulungu wace anali naye, namkuza kwakukuru.
2 Ndipo Solomo analankhula ndi Aisrayeli onse, ndi akuru a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga ali yense wa Israyeli, akuru a nyumba za makolo.
3 Ndipo Solomo ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibeoni; pakuti kumeneko kunali cihema cokomanako ca Mulungu adacimanga Mose mtumiki wa Yehova m'cipululu.
4 Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kucokera ku Kiriyati Yearimu kumka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.
5 Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezaleli mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la kacisi wa Yehova; ndipo Solomo ndi khamulo anafunako.
6 Nakwerako Solomo ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku cihema cokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza cikwi cimodzi.
7 Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomo, nati kwa iye, Pempha comwe ndikupatse.
8 Nati Solomo kwa Mulungu, Mwacitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwace.
9 Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akucuruka ngati pfumbi lapansi.
10 Mundipatse tsono nzeru ndi cidziwitso, kuti ndituruke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?
11 Ndipo Mulungu anati kwa Solomo, Popeza cinali mumtima mwako ici, osapempha cuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi cidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,
12 nzeru ndi cidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso cuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhala nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
13 Momwemo Solomo anadza ku Yerusalemu kucokera ku msanje uli ku Gibeoni, ku khomo la cihema cokomanako; ndipo anacita ufumu pa Israyeli.
14 Ndipo Solomo anasonkhanitsa magareta ndi apakavalo, nakhala nao magareta cikwi cimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magareta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.
15 Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golidi zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza icuruke ngati mikuyu yokhala kucidikha.
16 Ndi akavalo amene Solomo anali nao anafuma ku Aigupto; amalonda a mfumu anawalandira magulu magulu, gulu liri lonse mtengo wace.
17 Ndipo anatenga naturuka nalo gareta ku Aigupto mtengo wace masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wace zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawaturutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.