2 Mbiri 32 BL92

Sanakeribu agwera Yuda

1 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Sanakeribu mfumu ya Asuri, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.

2 Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Sanakeribu, ndi kuti nkhope yace inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndi Yerusalemu,

3 anapangana ndi akuru ace ndi amphamvu ace, kutseka madzi a m'akasupe okhala kunja kwa mudzi; namthandiza iwo.

4 Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asuri ndi kupeza madzi ambiri.

5 Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwace, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zocuruka.

6 Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye ku bwalo la ku cipata ca mudzi, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti,

7 Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena ku tenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asuri ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe acuruka koposa okhala naye;

8 pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anacirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.

9 Pambuyo pace Sanakeribu mfumu ya Asuri, akali ku Lakisi ndi mphamvu yace yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,

10 Atero Sanakeribu mfumu ya Asuri, Mutama ciani kuti mukhala m'linga m'Yerusalemu?

11 Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m'dzanja la mfumu ya Asuri?

12 Sanaicotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire ku guwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?

13 Simudziwa kodi comwe ine ndi makolo anga tacitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa?

14 Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga, kuti Mulungu wako adzakhoza kukulanditsa iwe m'dzanja mwanga?

15 Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe mulungu wa mtundu uli wonse wa anthu, kapena ufumu uli wonse, unakhoza kulanditsa anthu ace m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa?

16 Ndipo anyamata ace anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wace Hezekiya,

17 Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ace m'dzanja mwanga.

18 Ndipo anapfuula ndi mau akuru m'cinenedwe ca Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwabvuta, kuti alande mudziwu.

19 Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a pa dziko lapansi, ndiyo nchito ya manja a anthu.

20 Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ici, napfuulira Kumwamba.

21 Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, ku cigono ca mfumu ya Asuri. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi ku dziko lace. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wace, iwo oturuka m'matumbo mwace anamupha ndi lupanga pomwepo.

22 Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala m'Yerusalemu m'dzanja la Sanakeribu mfumu ya Asuri, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.

23 Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wace, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.

Nthenda ndi imfa ya Hezekiya

24 Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa cizindikilo codabwiza.

25 Koma Hezekiya sanabwezera monga mwa cokoma anamcitira, pakuti mtima wace unakwezeka; cifukwa cace unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.

26 Koma Hezekiya anadzicepetsa m'kudzikuza kwa mtima wace, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya.

27 Ndipo cuma ndi ulemu zinacurukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golidi, ndi timiyala ta mtengo wace, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma ziri zonse;

28 ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iri yonse, ndi makola a zoweta.

29 Nadzimangiranso midzi, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zocuruka; pakuti Mulungu adampatsa cuma cambirimbiri.

30 Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire ku madzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo nchito zace zonse.

31 Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babulo, amene anatumiza kwa iye kufunsira za codabwiza cija cidacitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwace.

32 Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi nchito zace zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.

33 Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ace, namuika polowerera ku manda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m'Yerusalemu anamcitira ulemu pa imfa yace. Ndipo Manase mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36