2 Mbiri 34 BL92

Yosiya acotsa cipembedzo ca mafano, nakonzanso Kacisi

1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu cimodzi.

2 Nacita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lace, osapambuka ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

3 Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lace; ndipo atakhala zaka khumi ndi cimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzicotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga,

4 Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pace; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.

5 Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a: nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.

6 Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efraimu, ndi Simeoni, mpaka Nafitali, m'mabwinja mwao mozungulira.

7 Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israyeli, nabwerera kumka ku Yerusalemu.

8 Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma safana mwana wa Azaliya, ndi Maseya kazembe wa mudzi, ndi Yona mwana wa Yoadazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wace.

9 Ndipo anadza kwa Hilikiya wansembe wamkulu, napereka ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira ku dzanja la Manase ndi Efraimu, ndi kwa otsala onse a Israyeli, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu.

10 Ndipo anazipereka m'dzanja la anchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa anchito akucita m'nyumba ya Yehova, kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;

11 anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.

12 Ndipo amunawo anacita nchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yohati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena ali yense wa luso la zoyimbira,

13 Anayang'aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira nchito ya utumiki uli wonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira.

Hilikiya apeza buku la cilamulo

14 Ndipo pakuturutsa ndarama zimene adalowa nazo ku nyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la cilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.

15 Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani.

16 Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzicita.

17 Nakhuthula ndarama zinapezeka m'nyumba ya Yehova, nazipereka m'manja a akapitao ndi m'manja a anchito.

18 Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

19 Ndipo kunali, atamva mfumu mau a cilamulo, anang'amba zobvala zace.

20 Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

21 Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israyeli ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukuru; popeza makolo athu sanasunga mau a Yehova kucita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.

Hulida aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu

22 Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasire wosunga zobvala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nanena naye mwakuti.

23 Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

24 Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo coipa, ndico matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda;

25 cifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.

26 Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kunena za mau udawamva,

27 popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzicepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ace otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzicepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zobvala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.

28 Taona, ndidzakusonkhanitsa ku makolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.

Yosiya ndi anthu acitanso pangano ndi Mulungu

29 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akulu akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.

30 Nikwera mfumu ku nyumba ya Yehova ndi amuna onse a m'Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse akuru ndi ang'ono; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a buku la cipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.

31 Ndipo mfumu inaimirira pokhala pace, nicita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda cotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, kucita mau a cipangano olembedwa m'bukumu.

32 Naimiritsapo onse okhala m'Yerusalemu ndi m'Benjamini. Ndipo okhala m'Yerusalemu anacita monga mwa cipangano ca Mulungu, Mulungu wa makolo ao.

33 Yosiya nacotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israyeli, natumikiritsa onse opezeka m'lsrayeli, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ace onse iwo sanapambuka kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36