2 Mbiri 9 BL92

Mfumu yaikazi ya ku Seba aceza ndi Solomo

1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo, anadza kumuyesera Solomo ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukuru, ndi ngamila zosenza zonunkhira, ndi golidi wocuruka, ndi timiyala ta mtengo wace; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.

2 Ndipo Solomo anammasulira mau ace onse, panalibe kanthu kombisikira Solomo, kamene sanammasulira.

3 Ndipo mfumu yaikazi ya ku Seba ataiona nzeru ya Solomo, ndi nyumba adaimanga,

4 ndi zakudya za pa gome lace, ndi makhalidwe a anyamata ace, ndi maimiriridwe a atumiki ace, ndi mabvalidwe ao, ndi otenga zikho ace, ndi mabvalidwe ao, ndi makweredwe ace pokwera iye kumka ku nyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.

5 Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m'dziko langa, ya macitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.

6 Koma sindinakhulupira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zocuruka; mwa, onjezatu pa mbiri ndidaimva.

7 Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima ciimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu.

8 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wacifumu wace, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ace; popeza Mulungu wanu anakonda Aisrayeli kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kucita ciweruzo ndi cilungamo.

9 Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wace; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Seba anapatsa mfumu Solomo.

10 Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomo otenga golidi ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.

11 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oyimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda.

12 Ndipo mfumu Solomo anampatsa mfumu yaikazi ya ku Seba cifuniro cace conse, ciri conse anacipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lace, iyeyu ndi anyamata ace.

Cuma ndi ulemerero wa Solomo

13 Kulemera kwace tsono kwa golidi anafika kwa Solomo caka cimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golidi;

14 osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golidi ndi siliva kwa Solomo.

15 Ndipo mfumu Solomo anapanga zikopa mazana awiri za golidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinathera golidi wonsansantha masekeli mazana awiri.

16 Napanganso malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinathera masekeli mazana atatu a golidi; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.

17 Mfumu inapanganso mpando wacifumu waukuru wa minyanga, naukuta ndi golidi woona.

18 Ndi mpando wacifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi copondapo mapazi cagolidi, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.

19 Ndi mikango khumi ndi iwiri Inaimirirapo, mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwa wotere m'ufumu uli wonse.

20 Ndipo zikho zomwera zonse za Solomo zinali zagolidi, ndi zipangizo zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali za golidi woona; siliva sanayesedwa kanthu m'masiku a Solomo.

21 Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golidi, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawanga mawanga.

22 Mamwemo mfumu Solomo inaposa mafumu onse a pa dziko lapansi, kunena za cuma ndi nzeru.

23 Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace Mulungu adazilonga m'mtima mwace.

24 Nabwera nao munthu yense mtulo wace, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolidi, zobvala, ndi zobvala za nkhondo, ndi zonunkhira, akavalo, ndi nyuru; momwemo caka ndi caka.

25 Ndipo Solomo anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magareta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'toidzi ya magareta, ndi m'Yerusalemu kwa mfumu.

26 Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Aigupto.

27 Ndipo mfumu inacurukitsa siliva m'Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu iri kumadambo kucuruka kwace.

28 Ndipo anakamtengera Solomo akavalo ku Aigupto, ndi ku maiko onse.

Kumwalira kwa Solomo

29 Macitidwe ena tsono a Solomo, oyamba ndi otsiriza, salembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobiamu mwana wa Nebati?

30 Ndipo Solomo anakhala mfumu ya Israyeli yense m'Yerusalemu zaka makumi anai.

31 Nagona Solomo pamodzi ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wace; ndipo Rehabiamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36