1 Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi,
2 ndipo anaturuka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
3 Masiku ambiri tsono Israyeli anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda cilamulo;
4 koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza.
5 Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakuturuka, kapena kwa iye wakulowa, koma mabvuto akuru anagwera onse okhala m'maikomo.
6 Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzace, ndi mudzi kupasula mudzi; pakuti Mulungu anawabvuta ndi masautso ali onse.
7 Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku nchito yanu kuli mphotho.
8 Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi cinenero ca Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nacotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efraimu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pa likole la Yehova.
9 Namemezaonse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ocokera ku Efraimu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ocuruka ocokera ku Israyeli, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wace anali naye.
10 Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu mwezi wacitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai.
11 Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.
12 Nalowa cipangano cakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;
13 ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israyeli aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkuru, wamwamuna kapena wamkazi.
14 Ndipo analumbira kwa Yehova ndi mau akuru, ndi kupfuula ndi mphalasa ndi malipenga.
15 Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi cifuno cao conse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.
16 Maaka yemwe, mai wace wa Asa, mfumu, anamcotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fano loopsa la Asera; ndipo Asa analikha fano lace, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kedroni.
17 Cinkana misanje siinacotsedwa m'Israyeli, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ace onse.
18 Ndipo analowa nazo zopatulika za atate wace, ndi zopatulika zace zace, ku nyumba ya Mulungu; ndizo siliva, ndi golidi, ndi zipangizo.
19 Ndipo panalibenso nkhondo mpaka Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zinai.