2 Mbiri 16 BL92

Asa apangana ndi Benihadadi, nalimbana ndi Israyeli

1 Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa, Basa mfumu ya Israyeli anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

2 Pamenepo Asa anaturutsa siliva ndi golidi ku cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,

3 Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wange ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golidi; mukani, pasulani pangano lanu ndi Basa mfumu ya Israyeli, kuti andicokere.

4 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ace a nkhondo ayambane ndi midzi ya Israyeli, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abelimaimu, ndi midzi yonse ya cuma ya Nafitali,

5 Ndipo kunali, pakumva ici Basa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa nchito yace.

6 Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yace, imene Basa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.

Hanani mlauli adzudzula Asa

7 Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, cifukwa cace khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.

8 Nanga Akusi ndi Alubi, sanakhala khamu lalikurukuru, ndi magareta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?

9 Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwacita copusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.

10 Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa mtima naye cifukwa ca ici. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.

11 Ndipo taonani, zocita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.

12 Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mpham bu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafuna Yehova, koma asing'anga.

13 Nagona Asa ndi makolo ace, namwalira atakhala mfumu zaka makumi anai.

14 Ndipo anamuika m'manda ace adadzisemerawo m'mudzi wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundu mitundu, monga mwa makonzedwe a osanganiza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36