2 Mbiri 12 BL92

Sisaki wa ku Aigupto athira nkhondo Rehabiamu

1 Ndipo kunacitika, utakhazikika ufumu wa Rehabiamu, nalimbika iye, anasiya cilamulo ca Yehova, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye.

2 Ndipo Rehabiamu atakhala mfumu zaka zinai, Sisaki mfumu ya ku Aigupto anakwerera Yerusalemu, popeza iwo adalakwira Yehova.

3 Anakwera ndi magareta cikwi cimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kuturuka m'Aigupto ngosawerengeka, Alubi, Asuki, ndi Akusi.

4 Ndipo analanda midzi yamalinga yokhala ya Yuda, nadza ku Yerusalemu.

5 Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehabiamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu cifukwa ca Sisaki, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, cifukwa cace Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisaki.

6 Pamenepo akalonga a Israyeli ndi mfumu anadzicepetsa, nati, Yehova ali wolungama.

7 Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzicepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzicepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa cipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisaki.

8 Koma adzakhala akapolo ace, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko.

Sisaki alanda cuma ca Kacisi ndi ca nyumba ya mfumu

9 Ndipo Sisaki mfumu ya Aigupto anakwerera Yerusalemu, nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; anazicotsa zonse; anacotsanso zikopa zagolidi adazipanga Solomo.

10 Ndipo Rehabiamu mfumu anapanga m'malo mwa izo zikopa zamkuwa, nazipereka m'manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

11 Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku cipinda ca olindirira.

12 Ndipo pakudzicepetsa iye mkwiyo wa Mulungu unamcokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma m'Yuda.

13 Nadzilimbitsa Rehabiamu mfumu m'Yerusalemu, nacita ufumu; pakuti Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, ndiwo mudzi Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli, kuikapo dzina lace; ndipo dzina la mace ndiye Naama M-amoni.

14 Koma anacita coipa, popeza sanalunjikitsa mtima wace kufuna Yehova.

15 Macitidwe ace tsono a Rehabiamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizilembedwa kodi m'buku la mau a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku onse.

16 Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide; ndipo Abiya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36