1 Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehabiamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisrayeli kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu.
2 Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,
3 Lankhula ndi Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,
4 Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense ku nyumba yace; pakuti cinthu ici cifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobiamu.
5 Ndipo Rehabiamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda.
6 Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekoa,
7 ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,
8 ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,
9 ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,
10 ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo midzi yamalinga ya m'Yuda ndi Benjamini.
11 Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi cakudya cosungikiratu, ndi mafuta, ndi lvinyo.
12 Ndi m'midzi iri yonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa cilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ace.
13 Ndipo ansembe ndi Alevi okhala m'Israyeli lonse anadziphatikiza kwa iye, ocokera m'malire ao Onse.
14 Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko ao ao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobiamu ndi ana ace anawataya, kuti asacitire Yehova nchito ya nsembe;
15 nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a ana a ng'ombe adawapanga.
16 Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ocokera m'mafuko onse a Israyeli, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.
17 Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehabiamu, mwana wa Solomo zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomo zaka zitatu.
18 Ndipo Rehabiamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliabu mwana wa Jese;
19 ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu.
20 Ndi pambuyo pace anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.
21 Ndipo Rehabiamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ace onse, ndi akazi ace ang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi ang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana akazi makumi asanu ndi limodzi).
22 Ndipo Rehabiamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkuru, kalonga mwa abale ace; ndiko kuti adzamlonga ufumu.
23 Ndipo anacita mwanzeru, nabalalitsa ana ace amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, ku midzi yonse yamalinga; nawapatsa cakudya cocuruka, nawafunira akazi ocuruka.