2 Mbiri 7 BL92

Cibvomerezo ca Yehova mwa moto ndi ulemerero wao wodzaza Kacisi

1 Atatha tsono Solomo kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi.

2 Ndipo ansembe sanakhoza kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

3 Ndi ana onse a Israyeli anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova panyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire.

4 Pamenepo mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.

5 Ndipo mfumu Solomo anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi, makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Yehova.

6 Naimirira ansembe m'udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoyimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala ciriri Israyeli yense.

7 Ndipo Solomo anapatula pakati pace pa bwalo liri pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomo linacepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta.

8 Nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye, khamu lalikuru ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Aigupto.

9 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu anacita msonkhano woletsa; popeza anacita zakupereka guwa la nsembe masiku asanu ndi awiri, ndi madyerero masiku asanu ndi awiri.

10 Ndipo tsiku la makumi awiri ndi citatu la mwezi wacisanu ndi ciwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao cifukwa ca zokoma Yehova adawacitira Davide, ndi Solomo, ndi Aisrayeli anthu ace.

Yehova aonekeranso kwa Solomo

11 Momwemo Solomo anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo ziri zonse zidalowa mumtima mwace mwa Solomo kuzicita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yace yace, anacita mosabwezeza.

12 Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomo usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.

13 Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;

14 ndipo anthu anga ochedwa dzina langa akadzicepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira coipa cao, ndi kuciritsa dziko lao.

15 Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga ochera, pemphero la m'malo ano.

16 Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba Iyi, kuti dzina langa likhaleko cikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.

17 Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga monga umo anayendera Davide atate wako, nukacita monga mwa zonse ndakulamulira iwe, nukasunga malemba anga ndi maweruzo anga;

18 pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu m'Israyeli.

19 Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu yina ndi kuilambira;

20 pamenepo ndidzawazula m'dziko langa limene ndinawapatsa; ndi nyumba yino ndinaipatulira dzina langa ndidzaitaya, osaionanso, ndi kuiyesa mwambi ndi mnyozo mwa mitundu yonse ya anthu.

21 Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yeliova ana tero ndi dziko lino ndi nyumba yino cifukwa ninji?

22 Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawaturutsa m'dziko la Aigupto, nagwira milungu yina, nailambira ndi kuitumikira; cifukwa cace anawagwetsera coipa ici conse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36