2 Mbiri 26 BL92

Uziyaagonjetsa adani ambiri

1 Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace Amaziya.

2 Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumu itagona ndi makolo ace.

3 Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.

4 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita atate wace Amaziya.

5 Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;

6 popeza anaturuka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.

7 Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala m'Guribaala, ndi Ameuni.

8 Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lace linabuka mpaka polowera ku Aigupto; pakuti analil mbika cilimbikire.

9 Uziya anamanganso nsanja m'Yerusalemu pa cipata ca kungondya, ndi pa cipata ca kucigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.

10 Namanga nsanja m'cipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi ku nthaka yopatsa bwino; pakuti ndiye mlimi.

11 Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, oturuka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeyeli, ndi kapitao Maseya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.

12 Ciwerengo conse ca akuru a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndico zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.

13 Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ocita nkhondo ndi mphamvu yaikuru, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.

14 Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zacitsulo, ndi maraya acitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.

15 Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungondya, aponye nao mibvi ndi miyala yaikuru. Ndi dzina lace linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwiza, mpaka analimbikatu.

Uziva alakwa ku Kacisi nasanduka wakhate

16 Koma atakhala wamphamvu, mtima wace unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wace; popeza analowa m'Kacisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la cofukiza.

17 Ndipo Azariya wansembe analowa pambuyo pace, ndi pamodzi naye ansembe a Yehova makumi asanu ndi atatu, ndiwo olimba mtima;

18 natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova, koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; turukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.

19 Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza iri m'dzanja lace kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pace, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo.

20 Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pace namkankhiza msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kuturukako, pakuti Yehova adamkantha.

21 Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa ku nyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wace anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.

22 Macitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amosi. Ndipo Uziya anagona ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36