2 Mbiri 2 BL92

Solomo apangana ndi Hiramu za mirimo ya Kacisi

1 Ndipo a Solomo anati alimangire dzina la Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wace.

2 Nawerenga Solomo amuna zikwi khumi mphambu makumi asanu ndi limodzi osenza mirimo, ndi amuna zikwi makumi asanu ndi atatu otema mitengo m'mapiri, ndi zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kuwayang'anira.

3 Ndipo Solomo anatumiza kwa Huramu mfumu ya Turo, ndi kuti, Monga momwe munacitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundicitire ine momwemo.

4 Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pace zonunkhira za pfungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wacikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa madyerero oikika a Yehova Mulungu wathu. Ndiwo macitidwe osatha m'Israyeli.

5 Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikuru; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkuru woposa milungu yonse.

6 Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira cofukiza ndiko?

7 Ndipo tsono munditumizire munthu wa luso lakucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota ziri zonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.

8 Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebano; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo m'Lebano; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu,

9 ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikuru ndi yodabwitsa.

10 Ndipo taonani, ndidzawapatsa anyamata anu otema akulikha mitengo miyeso ya tirigu wopuntha zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya barele zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikuru ya vinyo zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikufu ya mafuta zikwi makumi awiri.

11 Ndipo Huramu mfumu ya Turo anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomo, ndi kuti, Powakonda anthu ace Yehova anakulongani mfumu yao.

12 Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wace.

13 Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala Ralo, luntha, Huramu Abi,

14 ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana akazi a Dani, ndipo atate wace ndiye munthu wa ku Turo, wodziwa kucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira copanga ciri conse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.

15 Ndipo tsono tirigu ndi barele, mafuta ndi vinyo, mbuye wanga wanenazi, azitumize kwa anyamata ace;

16 ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebano monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.

17 Ndipo Solomo anawerenga alendo Onse okhala m'dziko la Israyeli, monga mwa mawerengedwe aja atate wace Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.

18 Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndilimodzi agwiritse anthu nchito.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36