1 Pamenepo anthu a m'dziko anatenga Yehoahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu m'Yerusalemu, m'malo mwa atate wace.
2 Yehoahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu.
3 Ndipo mfumu ya Aigupto anamcotsera ufumu wace m'Yerusalemu, nasonkhetsa dziko matalente zana limodzi a siliva, ndi talente limodzi la golidi.
4 Ndi mfumu ya Aigupto anamlonga Eliyakimu mng'ono wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lace likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehoahazi mkuru wace, namuka naye ku Aigupto.
5 Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi cimodzi, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wace.
6 Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babulo.
7 Nebukadinezara anatenganso zipangizo za nyumba ya Yehova kumka nazo ku Babulo, naziika m'kacisi wace ku Babulo.
8 Macitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zace anazicita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
9 Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nacita coipa pamaso pa Yehova.
10 Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babulo, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.
11 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi cimodzi,
12 nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wace; sanadzicepetsa kwa Yeremiya mneneri wakunena zocokera pakamwa pa Yehova.
13 Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lace, nalimbitsa mtima wace kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli,
14 Ndiponso ansembe akulu onse ndi anthu anacurukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene ana patula m'Yerusalemu.
15 Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo, ndi dzanja la mithenga yace, nalawirira mamawa kuituma, cifukwa anamvera cifundo anthu ace, ndi pokhala pace;
16 koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ace, naseka aneneri ace, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ace, mpaka panalibe colanditsa.
17 Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Akasidi, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osacitira cifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lace.
18 Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikuru ndi zazing'ono, ndi cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca mfumu, ndi ca akalonga ace, anabwera nazo zonsezi ku Babulo.
19 Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zace zonse zacifumu ndi moto, naononga zipangizo zace zonse zokoma.
20 Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babulo, nakhala iwo anyamata ace, ndi a ana ace, mpaka mfumu ya Perisiya idacita ufumu;
21 kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ace; masiku onse a kupasuka kwace linasunga sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.
22 Caka coyamba tsono ca Koresi mfumu ya Perisiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Koresi mfumu ya Perisiya, kuti abukitse mau m'ufumu wace wonse, nawalembenso, ndi kuti,
23 Atero Koresi mfumu ya Perisiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Ali yense mwa inu a anthu ace onse, Yehova Mulungu wace akhale naye, akwereko.