1 Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Yehoadana wa ku Yerusalemu.
2 Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosacita ndi mtima wangwiro.
3 Kunacitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ace amene adapha mfumu atate wace.
4 Koma sanapha ana ao, koma anacita monga umo mulembedwa m'cilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere chimo lace lace.
5 Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akuturukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi cikopa.
6 Analemberanso ngwazi zamphamvu za m'Israyeli zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente a siliva zana limodzi.
7 Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israyeli lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israyeli, sakhala ndi ana onse a Efraimu.
8 Koma ngati mumuka, citani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.
9 Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israyeli? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.
10 Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kucokera ku Efraimu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.
11 Nalimbika mtima Amaziya, natsogolera anthu ace, namuka ku Cigwa ca Mcere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.
12 Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, nawakankha pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.
13 Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betihoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.
14 Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yace, naigwadira, naifukizira,
15 Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu?
16 Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwacita ici ndi kusamvera kupangira kwanga.
17 Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani, tionane maso.
18 Ndi Yoasi mfumu ya Israyeli anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebano inapitapo, nipondereza mtungwi.
19 Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.
20 Koma wosamvera Amaziya, pakuti nca Mulungu ici kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.
21 Motero anakwera Yoasi mfumu ya Israyeli, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betisemesi, ndiwo wa Yuda.
22 Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israyeli, nathawa yense kuhema kwace.
23 Ndipo Yoasi mfumu ya Israyeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yoasi mwana wa Yehoahazi, ku Betisemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira cipata ca Efraimu kufikira cipata ca kungondya, mikono mazana anai.
24 Natenga golidi ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m'nyumba ya Mulungu kwa Obedi Edomu, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, acikole omwe; nabwerera kumka ku Samariya.
25 Ndipo Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yoasi mwana wa Yehoahazi mfumu ya Israyeli, zaka khumi ndi zisanu.
26 Macitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, salembedwa kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli?
27 Ndipo cipambukire Amaziya kusatsata Yehova, anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.
28 Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Yuda.