2 Mbiri 30 BL92

Hezekiya acita Paskha ku Yerusalemu

1 Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israyeli ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efraimu ndi Manase, kuti abwere ku nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha.

2 Pakuti mfumu idapangana ndi akuru ace, ndi msonkhano wonse wa m'Yerusalemu, kuti acite Paskha mwezi waciwiri.

3 Pakuti sanakhoza kumcita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikira, ndi anthu sadasonkhana ku Yerusalemu.

4 Ndipo cinthuci cinayenera m'maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse.

5 Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israyeli lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikuru sanacita monga mudalembedwa.

6 Tsono amtokoma anamuka ndi akalata ofuma kwa mfumu ndi akuru ace mwa Israyeli ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israyeli, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isake, ndi Israyeli, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asuri.

7 Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene anai akwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya,

8 Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ace opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kwa inu.

9 Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza cifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa cisomo ndi cifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye,

10 Ndipo amtokoma anapitira m'midzi m'midzi mwa dziko la Efraimu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.

11 Komatu ena a Aseri ndi Manase ndi a Zebuloni anadzicepetsa, nadza ku Yerusalemu.

12 Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kucita cowauza mfumu ndi akuru mwa mau a Yehova.

13 Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kucita madyerero a mkate wopanda cotupitsa mwezi waciwiri, msonkhano waukuru ndithu.

14 Ndipo anauka nacotsa maguwa a nsembe okhala m'Yerusalemu, nacotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kedroni.

15 Pamenepo anaphera Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi waciwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anacita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza ku nyumba ya Yehova.

16 Naima m'malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa cilamulo ca Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira ku dzanja la Alevi.

17 Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatula; potero Alevi anayang'anira kupha za Paskha kwa ali yense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova.

18 Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efraimu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretsa, koma anadya Paskha mosati monga munalembedwa.

19 Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense wakuika mtima wace kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ace, cinkana sanayeretsedwa monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.

20 Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawaciritsa anthu.

21 Ndipo ana a Israyeli opezeka m'Yerusalemu anacita madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe cacikuru; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoyimbira zakuliritsa kwa Yehova.

22 Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.

23 Ndipo msonkhano wonse unapangana kucita masiku asanu ndi awiri ena, nacita masiku asanu ndi awiri ena ndi cimwemwe.

24 Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe cikwi cimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akuru anapatsa msonkhano ng'ombe cikwi cimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembeambiri adadzipatula,

25 Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wocokera kwa Israyeli, ndi alendo ocokera ku dziko la Israyeli, ndi okhala m'Yuda, anakondwera.

26 Momwemo munali cimwemwe cacikuru m'Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Israyeli simunacitika cotero m'Yerusalemu.

27 Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pace popatulika Kumwamba.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36