2 Mbiri 35 BL92

Yosiya acita Paskha ku Yerusalemu

1 Pamenepo Yosiya anacitira Yehova Paskha m'Yerusalemu, naphera Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi woyamba.

2 Ndipo anaika ansembe pa udikiro wao, nawalimbikitsa acite utumiki wa nyumba ya Yehova.

3 Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisrayeli onse, ndiwo opatulima Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Israyeli anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ace Israyeli.

4 Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israyeli, ndi umo adalembera Solomo mwana wace.

5 Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.

6 Ndipo muphere Paskha, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kucita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.

7 Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, ana a nkhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paskha kwa ali yense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa cuma ca mfumu.

8 Ndi akulu ace anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehieli, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paskha.

9 Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netaneli, abale ace, ndi Hasabiya, ndi Yeyeli, ndi Yosabadi, akuru a Alevi, ana patsa Alevi zoweta zazing'ono zikwi zisanu, ndi ng'ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paskha.

10 Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m'zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu.

11 Pamenepo anaphera Paskha; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo.

12 Ndipo anacotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.

13 Ndipo anaoca Paskha pamoto, monga mwa ciweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.

14 Ndi pambuyo pace anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; cifukwa cace Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.

15 Ndi oyimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera

16 Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kucita Paskha, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.

17 Ndipo ana a Israyeli okhalako anacita Paskha nthawi yomweyo, ndi madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri.

18 Panalibe Paskha wocitika m'Israyeli wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samueli mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israyeli anacita Paskha wotere, ngati ameneyu anacita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisrayeli opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu.

19 Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anacita Paskha amene.

Yosiya ayambana ndi Neko mfumu ya Aigupto, naphedwa

20 Citatha ici conse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aigupto anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Firate; ndipo Yosiya anamturukira kuyambana naye.

21 Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndiri ndi ciani ndi inu, mfumu ya Yuda? sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndiri nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kubvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.

22 Koma Yosiya sanatembenuka nkhope yace kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ocokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'cigwa ca Megido.

23 Ndipo oponya anayang'anitsa mibvi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ace, Ndicotseni ndalasidwa ndithu.

24 Pamenepo anyamata ace anamturutsa m'gareta, namuika m'gareta waciwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ace. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.

25 Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oyimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israyeli; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro.

26 Macitidwe ena tsono a Yosiya, ndi nchito zace zokoma, monga mulembedwa m'cilamulo ca Yehova,

27 ndi zocita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36