2 Mbiri 29 BL92

Hezekiya mfumu ya Yuda

1 Hezekiya analowa ufumu wace ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Abiya mwana wa Zekariya.

2 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adacitira Davide kholo lace.

3 Caka coyamba ca ufumu wace, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso.

4 Nalowetsa ansembe ndi Alevi, nawasonkhanitsa pamalo poyera kum'mawa,

5 nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kucotsa zoipsa m'malo opatulika.

6 Pakuti analakwa makolo athu, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya cokhalamo Yehova, namfulatira.

7 Anatsekanso pa khomo la likole, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israyeli.

8 Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale codabwiza ndi cotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu.

9 Pakuti taonani, makolo athu adagwa ndi lupanga, ndi ana athu amuna ndi akazi ndi akazi athu ali andende cifukwa ca ici.

10 Tsono mumtima mwanga nditi ndicite cipangano ndi Yehova Mulungu wa Israyeli, kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kuticokera.

11 Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pace, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ace ndi kufukiza zonunkhira.

Alevi ayeretsa Kacisi

12 Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yoeli mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehaleleli; ndi a Agerisoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;

13 ndi a ana a Elizafana, Simri ndi Yeueli; ndi a ana a Asafu, Zekariya ndi Mataniya;

14 ndi a ana a Hemani, Yehudi ndi Simei ndi a ana a Yedutuni, Semaya ndi Uziyeli,

15 Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova.

16 Ndipo ansembe analowa m'kati mwace mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, naturutsira ku bwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza m'Kacisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuziturutsira kunja ku mtsinje wa Kedroni.

17 Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira ku likole la Yehova tsiku lacisanu ndi citatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi cisanu ndi cimodzi.

18 Pamenepo analowa m'katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zace zonse.

19 Zipangizo zonse zomwe adazitaya mfumu Ahazi m'ufumu wace m'kulakwa kwace kuja, tazikonza, ndi kuzipatula; ndipo taonani, ziri ku guwa la nsembe la Yehova.

Hezekiya aikanso cipembedzo ca Yehova

20 Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m'mudzi, nakwera kumka ku nyumba ya Yehova.

21 Ndipoanabweranazong'ombe zisanundi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yaucimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke pa guwa la nsembe la Yehova.

22 Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso ana a nkhosawo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe.

23 Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yaucimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao,

24 ndi ansembewo anawapha, nacita nsembe yaucimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kucita cotetezera Aisrayeli onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yaucimo zikhale za Aisrayeli onse.

25 Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ace.

26 Alevi tsono anaimirira ndi zoyimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga.

27 Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoyimbira za Davideyo mfumu ya Israyeli.

28 Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi oyimbira anayimba, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza.

29 Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.

30 Hezekiya mfumu ndi akalonga anauzanso Alevi ayimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anayimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.

31 Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika ku nyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.

32 Ndi kuwerenga kwace kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi ana a nkhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.

33 Ndi zinthu, zopatulika zinafikira ng'ombe mazana asanu ndi limodzi, ndi nkhosa zikwi zitatu.

34 Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha nchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula.

35 Ndiponso zidacuruka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iri yonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka.

36 Nakondwera Hezekiya ndi anthu onse pa ici Mulungu adakonzeratu; pakuti cinthuci cidacitika modzidzimutsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36