2 Mbiri 20 BL92

Yehosafati apempha Yehova pa Amoabu ndi Aamoni

1 Ndipo zitatha izi, kunacitika kuti ana a Moabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.

2 Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukuru wa anthu ocokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni Tamara, ndiwo Engedi.

3 Ndipo Yehosafati anacita mantha, nalunjikitsa nkhope yace kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.

4 Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anacokera ku midzi yonse ya Yuda kufuna Yehova.

5 Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, ku nyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;

6 nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu.

7 Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israyeli, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?

8 nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,

9 Cikatigwera coipa, lupanga, ciweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala ciriri pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kupfuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.

10 Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Moabu, ndi a ku phiri la Seiri, amene simunalola Israyeli awalowere, pakuturuka iwo m'dziko la Aigupto, koma anawapambukira osawaononga;

11 tapenyani, m'mene atibwezera; kudzatiinga m'colowa canu, cimene munatipatsa cikhale colowa cathu.

12 Mulungu wathu, simudzawaweruza? pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.

13 Ndipo Ayuda onse anakhala ciriri pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.

14 Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahazieli mwana wa Zekriya, mwana wa Benaya, mwana wa Yetieli, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano;

15 nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa cifukwa ca aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.

16 Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera cigwa cakuno ca cipululu ca Yerueli.

17 Si kwanu kucita nkhondo kuno ai; cirimikani, imani, nimupenye cipulumutso ca Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwaturukire, popeza Yehova ali ndi inu.

18 Ndipo Yehosafati anawerama mutu wace, nkhope yace pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.

19 Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mau omveketsa.

Amoahu ndi Aamoni akanthidwa

20 Nalawira mamawa, naturuka kumka ku cipululu ca Tekoa; ndipo poturuka iwo, Yehosafati anakhala ciriri, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m'Yerusalemu, Hmbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ace, ndipo mudzalemerera.

21 Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oyimbira Yehova, ndi kulemekeza ciyero cokometsetsa, pakuturuka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cosatha.

22 Ndipo poyamba iwo kuyimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.

23 Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana.

24 Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kucipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo iri ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.

25 Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ace kutenga zofunkha zao, anapezako cuma cambiri, ndi mitembo yambiri, ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinacuruka.

26 Ndi tsiku lacinai anasonkhana m'cigwa ca Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Beraka, mpaka lero lino.

27 Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kumka ku Yerusalemu ndi cimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.

28 Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, ku nyumba ya Yehova.

29 Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m'maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israyeli.

30 Nucita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wace anampumulitsira pozungulirapo.

31 Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la mace ndiye Azuba mwana wa Sili.

32 Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wace osapambukamo, nacita zoongoka pamaso pa Yehova.

33 Komatu misanje siinacotsedwa; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.

34 Macitidwe ena tsono adazicita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wochulidwa m'buku la mafumu a Israyeli.

35 Zitathaizi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israyeli, yemweyo anacita moipitsitsa;

36 naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisi, nazipanga zombozo m'Ezioni Gebere.

37 Pamenepo Eliezeri mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula nchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36