1 Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwace mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono khumi.
2 Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wace mikono isanu; ndi cingweca mikono makumi atatu cinalizunguniza.
3 Ndi pansi pace panali mafanziro a ng'ombe zakulizinga khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pace. Ng'ombezo zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.
4 Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwela, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana.
5 Ndi kucindikira kwace kunanga cikhato, ndi mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi zitatu.
6 Anapanganso mbiya zamphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.
7 Ndipo anapanga zoikapo nyali khumi zagolidi, monga mwa ciweruzo cace; naziika m'Kacisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.
8 Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kacisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolidi.
9 Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikuru, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zace ndi mkuwa.
10 Ndipo anaika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa cakumwela.
11 Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zace, ndi mbale zowazira zace. Natsiriza Huramu nchito adaicitira mfumu Solomo m'nyumba ya Mulungu:
12 nsanamira ziwiri, ndi zikhozo, ndi mitu iwiri inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi maukonde awiri akukuta zikho ziwiri za mitu iri pamwamba pa nsanamirazo,
13 ndi makangaza mazana anai a maukonde awiri wa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uli wonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo.
14 Anapanganso maphaka, napanga mbiya zamphwamphwa khumi pamwamba pa maphaka;
15 thawale limodzi ndi ng'ombe khumi ndi ziwiri pansi pace.
16 Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zace zonse, Huramu Abi anazipangira mfumu Solomo, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.
17 Mfumuyi inaziyenga pa cidikha ca ku Yordano, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.
18 Ndipo Solomo anazipanga zipangizo izi zonse zocurukadi, pakuti kulemera kwace kwa mkuwa sikunayeseka.
19 Solomo anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolidi lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;
20 ndi zoikapo nyali ndi nyali zace za golidi woona, zakuunikira monga mwa cilangizo cace cakuno ca moneneramo;
21 ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolidi, ndiwo golidi wangwiro;
22 ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golidi woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zace za m'katimo za malo opatulikitsa, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kacisi, zinali zagolidi.