2 Mbiri 5 BL92

1 Momwemo zidatha nchito zonse Solomo adazicitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo anabwera nazo zopatulika zija za atate wace Davide; naziika siliva, ndi golidi, ndi zipangizo zonse m'cuma ca nyumba ya Mulungu.Kuperekedwa kwa Kacisi.

2 Pamenepo Solomo anasonkhanitsira akulu akulu a Israyeli, ndi akuru onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israyeli, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la cipangano ca Yehova ku mudzi wa Davide ndiwo Zioni.

3 Ndipo amuna onse a Israyeli anasonkhana kwa mfumu kumadyerero anacitikawo, m'mwezi wacisanu ndi ciwiri.

4 Nadza akulu akulu onse a Israyeli, nanyamula likasalo Alevi.

5 Ndipo anakwera nalo likasa, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'cihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.

6 Ndi mfumu Solomo ndi khamu lonse la Israyeli losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kucuruka kwace.

7 Ndipo ansembe analowa nalo likasa la cipangano la Yehova kumalo kwace m'moneneramo mwa kacisi, m'malo opatulikitsa, pansi pa mapiko a akerubi.

8 Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pa malo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zace pamwamba pace.

9 Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa cakuno ca moneneramo, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo ziri komweko mpaka lero lino.

10 Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anacita cipangano ndi ana a Israyeli poturuka iwo m'Aigupto.

11 Ndipo ansembe anaturuka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;

12 Alevi omwe akuyimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao obvala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.

13 Ndipo kunali, pakucita limodzi amalipenga ndi oyimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoyimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti cifundo cace cikhala cikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;

14 ndipo ansembe sanakhoza kuimirira kutumikira cifukwa ca mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36