2 Mbiri 19 BL92

Mneneri Yehu adzudzula Yehosafati

1 Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera ku nyumba yace ku Yerusalemu mumtendere.

2 Naturuka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza oipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Cifukwa ca ici ukugwerani mkwiyo wocokera kwa Yehova.

3 Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazicotsa zifanizo m'dzikomo, mwaluniikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.

4 Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, naturukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efraimu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao.

5 Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, m'mudzi m'mudzi;

6 nati kwa oweruza, Khalani maso umo mucitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.

7 Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kucita; pakuti palibe cosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.

8 Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akuru a nyumba za makolo m'Israyeli, aweruzire Yehova, nanene mirandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.

9 Ndipo anawalangiza, ndi kuti, Muzitero ndi kuopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro.

10 Ndipo ukakudzerani mlandu uli wonse wocokera kwa abale anu okhala m'midzi mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa cilamulo ndi ciuzo, malemba ndi maweruzo, muwacenjeze kuti asaparamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzaparamula.

11 Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkuru, ndiye mkuru wanu m'mirandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismayeli, wolamulira nyumba ya Yuda, m'mirandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Citani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36