2 Mbiri 6 BL92

Conena Solomo ndi pemphero lace popereka Kacisi

1 Pamenepo Solomo anati, Yehova anati kuti adzakhala mu mdima wandiweyani.

2 Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.

3 Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yace, nidalitsa khamu lonse la Israyeli; ndi khamu lonse la Israyeli linaimirira.

4 Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, wakunena m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa: ndi manja ace, ndi kuti,

5 Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse m'mafuko onse a Israyeli, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu ali yense akhale kalonga wa anthu anga Israyeli;

6 koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israyeli.

7 Ndipo Davide atate wanga anafuna mumtima mwace kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

8 Koma Yehova anati kwa Davide atate wanga, Popeza unafuna mumtima mwako kulimangira dzina langa nyumba, unacita bwino kuti unatero mumtima mwako;

9 koma sudzandimangira nyumba ndiwe, koma mwana wako wakudzaturuka m'cuuno mwako, Iyeyo adzalimangira dzina langa nyumbayi.

10 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ace adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wacifumu wa Israyeli monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumbayi.

11 Ndipo ndalongamo likasa, muli cipangano ca Yehova, anacicita ndi ana a Israyeli.

12 Ndipo Solomo anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israyeli, natambasula manja ace.

13 Ndipo Solomo adapanga ciunda camkuwa, m'litali mwace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, ndi msinkhu wace mikono itatu, naciika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo, nagwada pa maondo ace pamaso pa khamu lonse la Israyeli, natambasulira manja ace kumwamba;

14 nati, Yehova. Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu ngati Inu, m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira cipangano ndi cifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;

15 inu amene mwasungira mtumiki wanu Davide atate wanga cija mudamlonjezaci: inde munanena ndi pakamwa panu, ndipo mwacita ndi dzanja lanu, monga momwe muli lero lino.

16 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'cilamulo canga, monga umo unayendera iwe pamaso panga.

17 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, acitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.

18 Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu pa dziko lapansi? taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?

19 Cinkana citero, labadirani pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kupfuula ndi kupempha kwace, kumene kapolo wanu apempha pamaso panu;

20 kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.

21 Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israyeli, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululikire.

22 Munthu akacimwira mnansi wace, ndipo akamuikira lumbiro lakumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira ku guwa lanu la nsembe, m'nyumba yino;

23 pamenepo mumvere m'Mwamba, nimucite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera chimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa cilungamo cace.

24 Ndipo anthu anu Israyeli akawakantha mdani cifukwa ca kukucimwirani, nakabwerera iwowa ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m'nyumba yino;

25 pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire chimo la anthu anu Israyeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

26 Mukatsekeka m'mwamba, mopanda mvula, cifukwa ca kukucimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa;

27 pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire chimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israyeli, mutawalangiza njira, yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale colowa cao.

28 Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala cinsikwi, kapena cinoni, dzombe, kapena kapuce; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la midzi yao; mukakhala mliri uli wonse, kapena nthenda iri yonse;

29 pemphero ndi pembedzero liri lonse likacitika ndi munthu ali yense, kapena ndi anthu anu onse Aisrayeli, akadziwa yense cinthenda cace, ndi cisoni cace, nakatambasulira manja ace kuloza ku nyumba iyi;

30 pamenepo mumvere m'Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera ali yense monga mwa njira zace zonse, monga mudziwa mtima wace; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;

31 kuti aope Inu, kuyenda m'njira zanu masiku onse akukhala iwo m'dziko limene munapatsa makolo athu.

32 Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israyeli, akafumira ku dziko lakutari cifukwa ca dzina lanu lalikuru, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono wanu wotambasuka; akadza iwowa ndi kupemphera kuloza ku nyumba iyi;

33 pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, nimumcitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisrayeli; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi ichedwa ndi dzina lanu.

34 Akaturukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iri yonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza ku mudzi uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu;

35 pamenepo mumvere m'Mwamba pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

36 Akacimwira Inu (pakuti palibe munthu wosacimwa), nimukakwiya nao, ndi kuwapereka kwa adani, kuti awatenge andende kumka nao ku dziko lakutali, kapena lapafupi;

37 koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tacimwa, tacita mphulupulu, tacita coipa;

38 akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m'dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mudzi mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi;

39 pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao; nimukhululukire anthu anu amene anakucimwirani.

40 Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale cipenyere, ndi makutu anu cimvere, pemphero locitika pamalo pano.

41 Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, abvale cipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.

42 Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukile zacifundo za Davide mtumiki wanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36