2 Mbiri 24 BL92

Yoasi akonzanso Kacisi

1 Yoasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mace ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

2 Ndipo Yoasi anacita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.

3 Ndipo Yehoyada anamtengera akazi awiri, nabala ana amuna ndi akazi.

4 Ndipo pambuyo pace mumtima mwa Yoasi munali cofuna kukonzanso nyumba ya Yehova.

5 Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Muturuke kumka ku midzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisrayeli onse ndarama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu caka ndi caka; ndipo inu fulumirani nayo nchitoyi. Koma Alevi sanafulumira nayo.

6 Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkuru wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kucokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israyeli, ukhale wa cihema ca umboni?

7 Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola citseko ca nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.

8 Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja ku cipata ca nyumba ya Yehova.

9 Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisrayeli m'cipululu.

10 Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha.

11 Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinacurukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhutula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwace. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zocuruka.

12 Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira nchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akucita ndi citsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.

13 Momwemo anacita ogwira nchito, nikula nchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ace, nailimbitsa.

14 Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golidi ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.

Anthu apatukira mafano

15 Koma Yehoyada anakalamba, nacuruka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.

16 Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anacita zabwino m'Israyeli, ndi kwa Mulungu, ndi ku nyumba yace.

17 Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.

18 Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, cifukwa ca kuparamula kwao kumene.

19 Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawacitira umboni; koma sanawamvera.

Zekariya adzudzula anthu naphedwa

20 Ndipo mzimu wa Mulungu unabvala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.

21 Koma anampangira ciwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.

22 Motero mfumu Yoasi sanakumbukila zokoma anamcitirazi Yehoyada atate wace, koma anapha mwana wace; ndiye pomwalira anati, Yehova acipenye, nacifunse.

23 Ndipo kunacitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.

24 Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikuru m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anacitira Yoasi zomlanga.

25 Ndipo atamcokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikuru), anyamata ace anamcitira ciwembu, cifukwa ca mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pace, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.

26 Omcitira ciwembu ndi awa: Zabadi, mwana wa Simeati wamkazi M-amoni; ndi Yozabadi, mwana wa Simiriti wamkazi Mmoabu.

27 Za ana ace tsono, ndi katundu wamkuru anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36