2 Mbiri 22 BL92

Ahaziya mfumu ya Yuda aphedwa ndi Yehu

1 Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wace wamng'ono akhale mfumu m'malo mwace; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kucigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda.

2 Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu caka cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Ataliya mwana wa Omri.

3 Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi mace acite coipa,

4 Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wace; ndi kuonongeka kwace nkumeneko.

5 Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, kukayambana nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.

6 Nabwerera iye kuti amcize ku Yezreeli, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaeli mfumu ya Aramu, Ndipo Azariya mwana wa Yehoramu mfumu yaYuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, popeza anadwala.

7 Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehocamu; pakuti atafika anaturukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimsi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

8 Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Israyeli, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.

9 Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wace wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.

Ataliya apha acifuma onse, Yoasi apulumuka

10 Pamene Ataliya anaona kuti mwana wace adafa, anauka, naononga mbeu yonse yacifumu ya nyumba ya Yuda.

11 Koma Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wace m'cipinda cogonamo. Momwemo Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wace wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.

12 Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi cimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36