2 Mbiri 10 BL92

Ufumu ugawanika pakati. Rehabiamu mfumu ya Yuda, Yerobiamu ya Israyeli

1 Ndipo Rehabiamu anamuka ku Sekemu; pakuti Aisrayeli onse adadza ku Sekemu kumlonga ufumu.

2 Ndipo kunali, atamva Yerobiamu mwana wa Nebati (popeza anali m'Aigupto kumene adathawira, kuthawa Solomo mfumu), Yerobiamu anabwera kucoka ku Aigupto.

3 Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobiamu ndi Aisrayeli onse, nalankhula ndi Rehabiamu, ndi kuti,

4 Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko nchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lace lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.

5 Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nacoka anthu.

6 Ndipo Rehabiamu mfumu anafunsana ndi akulu akulu, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?

7 Ndipo ananena naye, kuti, Mukawacitira cokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha.

8 Koma analeka uphungu wa akulu akuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pace.

9 Nati nao, Mundipangire bwanji inu, kuti tibwezere mau anthu awa ananena nanewo, ndi kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenzetsa ife?

10 Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.

11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

12 Tsono Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.

13 Ndipo mfumu inawayankha mokaripa, popeza mfumu Rehabiamu analeka uphungu wa akulu akulu,

14 nalankhula nao monga umo anampangira acinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

15 Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ace, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.

16 Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu, Aisrayeli inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisrayeli onse anamuka ku mahema ao.

17 Koma za ana a Israyeli okhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.

18 Pamenepo Rehabiamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israyeli anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehabiamu mfumu anafulumira kukwera pa gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.

19 Motero Israyeli anapandukana nayo nyumba ya Yuda mpaka lero lino.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36