2 Mbiri 8 BL92

Solomo amanga midzi yina

1 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yace yace,

2 Solomo anamanga midzi imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israyeli.

3 Ndipo Solomo anamuka ku Hamati Zoba, naugonjetsa.

4 Ndipo anamanga Tadimori m'cipululu, ndi midzi yonse yosungiramo cuma, imene anaimanga m'Hamati.

5 Anamanganso Betihoroni wa kumtunda, ndi Betihoroni wa kunsi, midzi ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;

6 ndi Balati, ndi midzi yonse yosungiramo cuma anali nayo Solomo, ndi midzi yonse ya magareta ace, ndi midzi ya apakavalo ace, ndi zonse anazifuna Solomo kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.

7 Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisrayeli,

8 mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israyeli sanawatha, mwa iwowa Solomo anawacititsa thangata mpaka lero lino.

9 Koma mwa ana a Israyeli Solomo sanawayesa akapolo omgwirira nchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ace akuru, ndi akuru a magareta ace, ndi apakavalo ace.

10 Amenewa anali akuru a akapitao a mfumu Solomo, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.

11 Ndipo Solomo anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israyeli; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.

Malongosoledwe a cipembedzo ndi nsembezo

12 Pamenepo Solomo anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo palikole,

13 monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa madyerero oikika, katatu m'caka, pa madyerero ali mkate wopanda cotupitsa, ndi pa madyerero a masabata, ndi pa madyerero a misasa.

14 Ndipo anaika monga mwa ciweruzo ca Davide atate wace zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku cipata ciri conse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.

15 Ndipo sanapambuka pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kali konse, kapena za cumaci.

16 Momwemo nchito yonse ya Solomo inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.

17 Pamenepo Solomo anamuka ku Ezioni Geberi, ndi ku Eloti pambali pa nyanja, m'dziko la Edomu.

18 Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amarinyero ace, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomo ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golidi, nabwera nao kwa Solomo mfumu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31 32 33 34 35 36