1 Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ace, naikidwa pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; ndi Yehoramu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
2 Ndipo anali nao abale ace, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehieli, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaeli, ndi Sefatiya, onsewa ndiwe ana a Yehosafati mfumu ya Israyeli.
3 Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikuru, za siliva, ndi za golidi, ndi za mtengo wace, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wace woyamba.
4 Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wace, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ace onse, ndi akalonga ena omwe a Israyeli,
5 Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nacita ufumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.
6 Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, umo anacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wace; ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova.
7 Koma Yehova sanafuna kuononga nyumba ya Davide cifukwa ca pangano adalicita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ace nyali nthawi zonse.
8 Masiku ace Aedomu anapanduka kucoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.
9 Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ace, ndi magareta ace onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magareta,
10 Cinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lace; cifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ace.
11 Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nacititsa okhala m'Yerusalemu cigololo, nakankhirako Ayuda.
12 Ndipo anamdzera kalata wofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayenda m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,
13 koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, ndi kucititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu cigololo, monga umo anacitira cigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;
14 taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi cuma canu conse, makanthidwe akuru;
15 ndipo mudzadwala kwakukuru nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzaturuka cifukwa ca nthendayi tsiku ndi tsiku.
16 Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;
17 ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda cuma conse cinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ace omwe, ndi akazi ace, osamsiyira mwana, koma Yehoahazi yekha mwana wace wamng'ono.
18 Ndi pambuyo pace pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m'matumbo ace ndi nthenda yosacira nayo.
19 Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pace pa zaka ziwiri, anaturuka matumbo ace mwa nthenda yace namwalira nazo nthenda zoipa, Ndipo anthu ace sanampserezera zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ace.
20 Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.