1 Ndipo caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yerobiamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.
2 Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la mace ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyeli wa ku Gibeya. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.
3 Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobiamu atandandalitsa nkhondo yace ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.
4 Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efraimu, nati, Mundimvere Yerobiamu ndi Aisrayeli onse;
5 simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka ciperekere ufumu wa Israyeli kwa Davide, kwa iye ndi ana ace, ndi pangano la mcere?
6 Koma Yerobiamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomo mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wace.
7 Ndipo anamsonkhanira amuna acabe, anthu opanda pace, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehabiamu mwana wa Solomo, muja Rehabiamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka.
8 Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu ana a ng'ombe agolidi adawapanga Yerobiamu akhale milungu yanu.
9 Simunapitikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amacita anthu a m'maiko ena? kuti ali yense wakudza kudzipatulira ndi mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.
10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tiri nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi. Alevi, m'nchito mwao,
11 nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za pfungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi coikapo nyali cagolidi ndi nyali zace, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga cilangizo ca Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.
12 Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ace, ndi malipenga oliza nao cokweza, kukulizirani inu cokweza. Ana a Israyeli inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.
13 Koma Yerobiamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.
14 Ndipo poceuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; napfuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.
15 Pamenepo amuna a Yuda anapfuula cokweza; ndipo popfuula amuna a Yuda, kunacitika kuti Mulungu anakantha Yerobiamu ndi Aisrayeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.
16 Ndipo ana a Israyeli anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao.
17 Ndipo Abiya ndi anthu ace anawakantha makanthidwe akuru; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazanaasanu a Israyeli.
18 Momwemo anacepetsedwa ana a Israyeli nthawi ija, nalakika ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.
19 Ndipo Abiya analondola Yerobiamu, namlanda midzi yace, Beteli ndi miraga yace, ndi Yesana ndi miraga yace, ndi Efroni ndi miraga yace.
20 Ndi Yerobiamu sanaonanso mphamvu m'masiku a Abiya, namkantha Yehova, wa iye.
21 Koma Abiya anakula mphamvu, nadzitengera akazi khumi ndi anai, nabala ana amuna makumi awiri mphambu awiri, ndi ana akazi khumi mphambu asanu ndi mmodzi.
22 Macitidwe ena tsono a Abiya, ndi mayendedwe ace, ndi mau ace, alembedwa m'buku lomasulira la mneneri Ido.