1 Ndipo Yehosafati mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israyeli.
2 Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efraimu, imene adailanda Asa atate wace.
3 Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zace zoyamba za kholo lace Davide, osafuna Abaala;
4 koma anafuna Mulungu wa kholo lace nayenda m'malamulo ace, osatsata macitidwe a Israyeli.
5 Cifukwa cace Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lace, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamcurukira cuma ndi ulemu.
6 Ndi mtima wace unakwezeka m'njira za Yehova; anacotsanso misanje ndi zifanizo m'Yuda.
7 Caka cacitatu ca ufumu wace anatuma akalonga ace, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netaneli, ndi Mikaya, aphunzitse m'midzi ya Yuda;
8 ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asaheli, ndi Semiramoti, ndi Yonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yoramu, ansembe.
9 Ndipo anaphunzitsa m'Yuda ali nalo buku la cilamulo la Yehova, nayendayenda m'midzi yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.
10 Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambana ndi Yehosafati.
11 Ndipo Afilisti ena anabweca nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.
12 Ndipo Yehosafati anakula cikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya cuma.
13 Nakhala nazo nchito zambiri m'midzi ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu m'Yerusalemu.
14 Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akuru a zikwi; Adina wamkuru, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;
15 ndi wotsatana naye mkuru Yohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;
16 ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri;
17 ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;
18 wotsatana naye Yozabadi, ndi pamodzi ndi iye okonzekeratu ku nkhondo zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.
19 Ndiwo amene analindirira mfumu, osawerenga iwo aja mfumu adawaika m'midzi yamalinga m'Yuda monse.