1 Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yeroamu, ndi Ismayeli mwana wa Yohanana, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.
2 Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'midzi yonse ya Yuda, ndi akuru a nyumba za makolo m'Israyeli; nadza iwo ku Yerusalemu.
3 Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.
4 Cimene muzicita ndi ici: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera dzuwa la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;
5 ndi limodzi la magawo atatu likhale ku nyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku cipata ca maziko; ndi anthu onse akhale m'mabwalo a nyumba ya Yehova.
6 Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.
7 Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zace m'dzanja mwace; ndipo ali yense wolowa m'nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakuturuka iye.
8 Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anacita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ace alowe dzuwa la Sabata pamodzi ndi oturuka dzuwa la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasula zigawo.
9 Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi maraya acitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba, ya Mulungu.
10 Ndipo anaika anthu onse, yense ndi cida cace m'dzanja lace, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya ku dzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya ku dzanja lamanzere la nyumba, kuloza ku guwa la nsembe ndi kunyumba.
11 Pamenepo anaturutsa mwana wa mfumu, nambveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ace anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.
12 Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;
13 napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yace polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oyimbira omwe analiko ndi zoyimbirazo, nalangiza poyimbira colemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, nati, Ciwembu, ciwembu.
14 Koma Yehoyada wansembe anaturuka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mturutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo ali yense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova.
15 Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku cipata ca akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.
16 Ndipo Yehoyada anacita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.
17 Ndi anthu onse anamuka ku nyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ace a nsembe, ndi mafano ace; namupha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe.
18 Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, ndi kukondwera ndi kuyimbira, monga mwa cilangizo ca Davide.
19 Ndipo anaika odikira ku makomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kali konse asalowemo.
20 Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu ku nyumba ya Yehova; nalowera pa cipata ca kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.
21 Ndipo anthu onse a m'dziko anakondwera; ndi m'mudzi munali cete, atamupha Ataliya ndi lupanga.