1 Ndipo mfumu Solomo anakonda akazi ambiri acilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Moabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Zidoni, ndi Ahiti;
2 a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israyeli za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomo anawaumirira kuwakonda.
3 Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana akazi a mafumu, ndi akazi acabe mazana atatu; ndipo akazi ace anapambutsa mtima wace.
4 Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ace anapambutsa mtima wace atsate milungu yina; ndipo mtima wace sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide atate wace.
5 Tsono Solomo anatsata Asitoreti fano la anthu a Zidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni.
6 Ndipo Solomo anacita coipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wace.
7 Pamenepo Salomo anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amoabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri liri patsogolo pa Yerusalemu.
8 Ndipo momwemo anacitiranso akazi ace onse acilendo, amene amafukizira naphera nsembe mafano ao.
9 Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomo, pokhala mtima wace unapambuka kwa Yehova Mulungu wa Israyeli, amene adamuonekera kawiri,
10 namlamulira za cinthu comweci, kuti asatsate milungu yina; koma iye sanasunga cimene Yehova anacilamula.
11 Cifukwa cace Yehova ananena ndi Solomo, Popeza cinthu ici cacitika ndi iwe, ndipo sunasunga cipangano canga ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung'ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako.
12 Koma m'masiku ako sindidzatero cifukwa ca Davide atate wako, koma ndidzaung'ambira m'manja mwa mwana wako;
13 komatu sindidzacotsa ufumu wonsewo; pfuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi cifukwa ca Yerusalemu amene ndinamsankha.
14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomo mdani, ndiye Hadadi M-edomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu.
15 Pakuti pamene Davide adali m'Edomu, ndipo Yoabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse m'Edomu;
16 pakuti Yoabu ndi Aisrayeli onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse m'Edomu;
17 Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wace pamodzi naye, kumka ku Aigupto, Hadadiyo akali mwana.
18 Ndipo anacoka ku Midyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Aigupto kwa Farao mfumu ya Aigupto, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.
19 Ndipo Farao anamkomera mtima ndithu Hadadiyo, nampatsa mkazi ndiye mbale wa mkazi wace, mbale wace wa Takipenesi mkazi wamkulu wa mfumu.
20 Ndipo mbale wa Takipenesi anamuonera Genubati mwana wace, ameneyo Takipenesi anamletsera kuyamwa m'nyumba ya Farao, ndipo Genubati anakhala m'banja la Farao pamodzi ndi ana amuna a Farao.
21 Ndipo atamva Hadadi ku Aigupto kuti Davide anagona ndi makolo ace, ndi kuti Yoabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.
22 Tsono Farao anati kwa iye, Koma cikusowa iwe nciani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.
23 Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wace Hadadezeri mfumu ya ku Zoba.
24 Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, hakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.
25 Ndipo iye anali mdani wa Israyeli masiku onse a Solomo, kuonjezerapo coipa anacicita Hadadi, naipidwa nao Aisrayeli, nakhala mfumu ya ku Aramu.
26 Ndipo Yerobiamu mwana wa Nebati M-efrati wa ku Zereda mnyamata wa Solomo, dzina la amace ndiye Zeruwa, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lace pa mfumu.
27 Ndipo cifukwa cakukweza iye dzanja lace pa mfumu ndi cimeneci: Solomo anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wace.
28 Ndipo munthu ameneyo Yerobiamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomo anamuona mnyamatayo kuti ngwacangu, anamuika akhale woyang'anira wa nchito yonse ya nyumba ya Yosefe.
29 Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobiamu anaturuka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anabvaliratu cobvala catsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo.
30 Ndipo Ahiyayo anagwira cobvala cace catsopano, nacing'amba khumi ndi pawiri.
31 Nati kwa Yerobiamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taona ndidzaung'amba ufumu m'dzanja la Solomo ndi kukupatsa iwe mafuko khumi.
32 Koma iye adzakhala nalo pfuko limodzi, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi ca Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israyeli.
33 Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Azidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amoabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kucita cimene ciyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wace.
34 Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lace, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ace onse, cifukwa ca Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, cifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.
35 Koma ndidzalanda ufumu m'dzanja la mwana wace, ndi kupatsa iwe mafuko khumi amene.
36 Ndipo ndidzamninkha mwana wace pfuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale cikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.
37 Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzacita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israyeli.
38 Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kucita cilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga nelinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israyeli.
39 Ndipo cifukwa ca ici nelidzazunza mbumba ya Davide, koma si masiku onse ai.
40 Cifukwa cace Solomo anafuna kupha Yerobiamu, ndipo Yerobiamu anathawira ku Aigupto kwa Sisaki mfumu ya Aigupto, nakhala m'Aigupto kufikira imfa ya Solomo.
41 Ndipo macitidwe otsiriza a Solomo, ndi nchito zace zonse anazicita, ndi nzeru zace, kodi sizilembedwa zimenezo m'buku la madtidwe a Solomo?
42 Ndipo masiku amene Solomo anakhala mfumu ya Aisrayeli onse m'Yerusalemu anali zaka makumi anai.
43 Ndipo Solomo anagona ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wace; ndipo Rehabiamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.