1 Mafumu 19 BL92

Eliya athawa Yezebeli

1 Ndipo Ahabu anauza Yezebeli zonse anazicita Eliya, ndi m'mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo,

2 Tsono Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe yino.

3 Ndipo iye ataona cimeneci, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wace pamenepo.

4 Koma iye mwini analowa m'cipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, cotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindiri wokoma woposa makolo anga.

5 Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.

6 Ndipo anaceuka, naona kumutu kunali kamkate kooca pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi,

7 Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kaciwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakulaka.

8 Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvuya cakudya cimeneco masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika ku phiri la Mulungu ku Horebu.

Eliya ku phiri la Horebu

9 Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Ucitanji pano, Eliya?

10 Ndipo anati, Ine ndinacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli anasiya cipangano canu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.

11 Ndipo iye anati, Turuka, nuime pa phiri tino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikuru ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhala m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali cibvomezi; komanso Yehova sanali m'cibvomezico.

12 Citaleka cibvomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo, Utaleka mota panali bata la kamphepo kayaziyazi.

13 Ndipo atamva Eliya, anapfunda nkhope yace ndi copfunda cace, naturuka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Ucitanji kuno, Eliya?

14 Nati iye, Ndacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli ataya cipangano canu, nagumula maguwa a nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.

15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kucipululu kumka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaeli akhale mfumu ya Aramu;

16 ukadzozenso Yehu mwana wa Nimsi akhale mfumu ya Israyeli; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abelimehola akhale mneneri m'malo mwako.

17 Ndipo kudzacitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaeli; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu,

18 Ndiponso ndidasiya m'lsrayeli anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampso-mpsona ndi milomo yao.

19 Tsono anacokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa cikhasu ng'ombe ziwiri ziwiri magori khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa gori lakhumi ndi ciwiri; ndipo Eliya anamka kunali iyeyo, naponya copfunda cace pa iye.

20 Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndithange ndakapsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera, ndakucitanji?

21 Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yace ndi zipangizo za zocitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22