1 Mafumu 16 BL92

Yehu aneneratu kugwa kwa Basa

1 Ndipo mau a Yehova akutsutsa Basa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati,

2 Popeza ndinakukuza iwe kucokera kupfumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israyeli, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi kucimwitsa anthu anga Israyeli, kuputa mkwiyo wanga ndi macimo ao;

3 taona, ndidzacotsa psiti Basa ndi nyumba yace, ndipo ndidzafanizitsa nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati,

4 Agaru adzadya ali yense wa Basa amene adzafera m'mudzi, ndipo amene adzafera m'thengo zidzamudya mbalame za m'mlengalenga.

5 Tsono macitidwe ena a Basa, ndi nchito zace, ndi mphamvu zace, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

6 Nagona Basa ndi makolo ace, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

7 Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Basa ndi nyumba yace, cifukwa ca zoipa zonse anazicita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wace ndi macitidwe a manja ace, nafanana ndi nyumba ya Yerobiamu; ndiponso popeza anaikantha.

Ela, Zimri, ndi Omri, mafumu a Israyeli

8 Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa analowa ufumu wa Israyeli ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.

9 Ndipo mnyamata wace Zimri, ndiye woyang'anira dera lina la magareta ace, anampangira ciwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.

10 Nalowamo Zimri, namkantha, namupha caka ca makomi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.

11 Ndipo kunali, atalowa ufumu wace, nakhala pa mpando wacifumu wace, anawakantha onse a m'nyumba ya Basa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ace, kapena wa mabwenzi ace.

12 Motero Zimri anaononga nyumba yonse ya Basa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Basa, mwa dzanja la Yehu mneneri,

13 cifukwa ca macimo onse a Basa, ndi macimo a Ela mwana wace anacimwawo, nacimwitsa nao Aisrayeli, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli ndi zacabe zao.

14 Tsono macitidwe ena a Ela, ndi nchito zace zonse, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

15 Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, Zimri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.

16 Koma anthu aja omangira misasa anamva kuti Zimri wacita ciwembu, nakanthanso mfumu; cifukwa cace tsiku lomwelo Aisrayeli onse a kumisasa anamlonga Omri kazembe wa nkhondo akhale mfumu ya Israyeli.

17 Ndipo Omri anacoka ku Gibetoni, ndi Aisrayeli onse naye, nakamangira misasa Tiriza.

18 Kunali tsono, pakuona Zimri kuti nkhondo yalowa m'mudzi, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi mota nyumba ya mfumu, nafa;

19 cifukwa ca macimo ace anacimwawo, pakucita coipa pamaso pa Yehova; popeza anayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi m'chimo lace anacimwa nalolo, nacimwitsa nalo Aisrayeli.

20 Macitidwe ena tsono a Zimri, ndi ciwembu anacicitaco, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

21 Pamenepo anthu a Israyeli anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omri.

22 Koma anthu akutsata Omri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omri nakhala mfumu.

23 Caka ca makumi atatu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Omri anayamba kukhala mfumu ya Israyeli, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi cimodzi.

24 Ndipo anagula kwa Semeri citunda ca Samaria ndi matalente awiri a siliva, namanga pacitundapo, nacha dzina lace la mudzi anaumanga Samaria, monga mwa dzina la Semeri mwini citundaco.

25 Koma Omri anacimwa pamaso pa Yehova, nacita zoipa koposa onse adamtsogolerawo.

26 Nayenda m'njira yonse ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi chimo lace anacimwitsa nalo Aisrayeli, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli ndi zacabe zao.

27 Ndipo macitidwe ena a Omri anawacita, ndi mphamvu yace anaionetsa, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

28 Nagona Omri ndi makolo ace, naikidwa m'Samaria; ndipo Ahabu mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

Ahabu mfumu yoipa ya Israyeli

29 Ndipo caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omri analowa ufumu wa Israyeli, nakhala Ahabu mwana wa Omri mfumu ya Israyeli m'Samaria zaka makumi awiri mphambu ziwiri.

30 Ndipo Ahabu mwana wa Omri anacimwa pamaso pa Yehova koposa onse adamtsogolerawo.

31 Ndipo kunali monga ngati kunamcepera kuyenda m'macimo a Yerobiamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebeli mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Azidoni, natumikira Baala, namgwadira,

32 Nammangira Baala guwa la nsembe m'nyumba ya Baala anaimanga m'Samaria.

33 Ahabu anapanganso cifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israyeli adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli,

34 M'masiku ace Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko; pokhazika maziko ace anadzifetsera Abiramu mwana wace woyamba, poimika zitseko zace anadzifetsera Zegubi mwana wace wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22