2 Samueli 21 BL92

Njala m'dziko, cifukwa cace, matsirizidwe ace

1 Ndipo m'masiku a Davide munali odala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndico cifukwa ca Sauli ndi nyumba yace yamwazi, popeza iye anawapha Agibeoni.

2 Ndipo mfumu inaitana Agibeoni, ninena nao (koma Agibeoni sanali a ana a Israyeli, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israyeli anawalumbirira kwa iwo, koma Sauli anafuna kuwapha mwa cangu cace ca kwa ana a Israyeli ndi a Yuda).

3 Ndipo Davide ananena ndi Agibeoni, Ndidzakucitirani ciani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi ciani kuti mukadalitse colowa ca Yehova?

4 Ndipo Agibeoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golidi wa Sauli kapena nyumba yace; ndiponso sitifuna kupha munthu ali yense wa m'Israyeli. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakucitirani.

5 Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife cotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israyeli,

6 mutipatse ana ace amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapacika kwa Yehova m'Gibeya wa Sauli, wosankhika wa Yehova, Mfumu niti, Ndidzawapereka.

7 Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, cifukwa ca lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Jonatani mwana wa Sauli.

8 Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Sauli, ndiwo Arimoni ndi, Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, amene iye anambalira Adriyeli mwana wa Barizilai Mmeholati;

9 niwapereka m'manja a Agibeoni, iwo nawapacika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kuceka barele.

10 Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga ciguduli, nadziyalira ici pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ocokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zirombo za kuthengo usiku.

11 Ndipo anauza Davide cimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Sauli anacita.

12 Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace kwa anthu a ku Jabezi Gileadi amene anawaba m'khwalala la Betisani, kumene Afilisti adawapacika, tsiku lija Afilistiwo anapha Sauli ku Giliboa;

13 nacotsa kumeneko mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapacikidwa.

14 Naika mafupa a Sauli ndi Jonatani mwana wace ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wace; nacita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pace Mulungu anapembedzeka za dzikolo.

Nkhondo zakupha ziphona za Afilisti

15 Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisrayeli; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ace pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

16 Ndipo Isibenobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wace kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anabvala lupanga latsopano, nati aphe Davide.

17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfliistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzaturuka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israyeli.

18 Ndipo kunali citapita ici, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.

19 Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elhanani mwana wa Jare-oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliate Mgiti, amene mtengo wa mkondo wace unanga mtanda wa woombera nsaru.

20 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukuru, amene anali nazo zala zisanu ndi cimodzi pa dzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi cimodzi kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.

21 Ndipo pakutonza Israyeli iyeyu, Jonatani mwana wa Simeyi mbale wa Davide anamupha.

22 Awa anai anawabala ndi Rafa, ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24