1 Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba cilimbire, ndi nyumba ya Sauli inafoka cifokere.
2 Ndipo ana a Davide anabadwira ku Hebroni. Mwana woyamba ndiye Amnoni, wa Ahinoamu wa ku Jezreeli;
3 waciwiri Kileabu, wa Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli; ndi wacitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;
4 ndi wacinai Adoniya mwana wa Hagiti; ndi wacisanu Sefatiya mwana wa Abitali;
5 ndi wacisanu ndi cimodzi Itireamu wa Egila mkazi wa Davide. Awa anambadwira Davide ku Hebroni.
6 Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide, Abineri analimbikira nyumba ya Sauli.
7 Ndipo Sauli adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lace ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga?
8 Pomwepo Abineri anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa gam wa Yuda kodi? Lero lino ndirikucitira zokoma nyumba ya Sauli atate wanu, ndi abale ace, ndi abwenzi ace, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu.
9 Mulungu alange Abineri, naonjezepo, ndikapanda kumcitira Davide monga Yehova anamlumbirira;
10 kucotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazika mpando wadfumu wa Davide pa Israyeli ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
11 Ndipo iye sanakhoza kuyankha Abineri mau amodzi cifukwa ca kumuopa iye.
12 Ndipo Abineri anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisrayeli onse atsate inu.
13 Nati iye, Cabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira cinthu cimodzi, ndico kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Sauli, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.
14 Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Sauli, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.
15 Pomwepo Isiboseti anatumiza namcotsera kwa mwamuna wace, kwa Palitieli mwana wa Laisi.
16 Ndipo mwamuna waceyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Baburimu. Pomwepo Abineri ananena naye, Coka, bwerera; ndipo anabwerera.
17 Ndipo Abineri analankhula nao akuru a Israyeli nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu;
18 citani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, a Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisrayeli ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.
19 Ndipo Abineri analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abineri anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisrayeli ndi a nyumba yonse ya Benjamini.
20 Abineri nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abineri ndi anthu okhala naye madyerero.
21 Pomwepo Abined anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisrayeli onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Comweco Davide analawirana ndi Abineri, namuka iye mumtendere.
22 Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yoabu anabwera kucokera ku nkhondo yobvumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abineri sanali ku Hebroni kwa Davide, cifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.
23 Tsono pofika Yoabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yoabu nati, Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendereo
24 Pomwepo Yoabu anadza kwa mfumu, nati, Mwacitanji? Taonani, Abineri anadza kwa inu, cifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti acokedi.
25 Mumdziwa Abineri mwana wa Neri kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kuturuka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikucita inu.
26 Ndipo Yoabu anaturuka kwa Davide, natumizira Abineri mithenga, amene anambweza ku citsime ca Sira. Koma Davide sanacidziwa.
27 Pofikanso Abineri ku Hebroni, Yoabu anampambutsa kupita nave pakati pa cipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, cifukwa ca mwazi wa Asaheli mbale wace.
28 Ndipo pambuyo pace, pakucimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osacimwira mwazi wa Abineri mwana wa Neri, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;
29 cilango cigwere pa mutu wa Yoabu ndi pa nyumba yonse ya atate wace; ndipo kusasoweke ku nyumba ya Yoabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa cakudya.
30 Motero Yoabu ndi Abisai mbale wace adapha Abineri, popeza iye adapha mbale wao Asaheli ku Gibeoni, kunkhondo.
31 Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zobvala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'cuuno, nimulire Abineri. Ndipo mfumu Davide anatsata cithatha.
32 Ndipo anaika Abineri ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ace nilira ku manda a Abineri, nalira anthu onse.
33 Ndipo mfumu inanenera Abineri nyimbo iyi ya maliro, niti,Kodi Abineri anayenera kufa ngati citsiru?
34 Manja anu sanamangidwa, mapazi anu sanalongedwa m'zigologolo;Monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu.Ndipo anthu onse anamliranso.
35 Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide cakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
36 Ndipo anthu onse anacisamalira, ndipo cinawakomera; ziri zonse adazicita mfumu zidakomera anthu onse.
37 Momwemo anthu onse ndi Aisrayeli onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumira kwa mfumu kupha Abineri mwana wa Neri.
38 Ndipo mfumu inati kwa anyamata ace, Simudziwa kodi kuti kalonga, ndi munthu womveka, wagwa lero m'Israyeli?
39 Ndipo ndikali wofoka ine lero, cinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wocita coipa monga mwa coipa cace.