1 Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.
2 Ndipo Yoabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nubvale zobvala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikuru.
3 Nulowe kwa mfumu, nulankhule nayo monga momwemo. Comweco Yoabu anampangira mau.
4 Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yace pansi namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.
5 Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga ana mwalira.
6 Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwa analimbana kumunda, panaboo wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzace namupha.
7 Ndipo onani, cibale conse cinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wace, kuti timuphe cifukwa ca moyo wa mbale wace amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; comweco adzazima khara langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.
8 Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita ku nyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe.
9 Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wacifumu wao zikhale zopanda cifukwa.
10 Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine ali yense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.
11 Nati iye, Mfumu mukumbukile Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
12 Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti Iyo, Nena.
13 Ndipo mkaziyo anati, Cifukwa ninjinso munalingalira cinthu cotere pa anthu a Mulungu? pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga woparamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wace.
14 Pakuti kufa tidzafa, ndipo tiri ngati madzi otayika pansi amene sakhoza kuwaolanso; ngakhale Mulungu sacotsa moyo, koma alingalira ngra yakuti wotayikayo asakhale womtayikira iye.
15 Cifukwa cace tsono cakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndico kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzacita copempha mdzakazi wace.
16 Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wace m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kuticotsa ku colowa ca Mulungu.
17 Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
18 Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.
19 Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yoabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yoabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.
20 Mnyamata wanu Yoabu anacita cinthu ici kuti asandulize mamvekedwe a mranduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse ziri m'dziko lapansi.
21 Ndipo mfumuyo inanena ndi Yoabu, Taonatu, ndacita cinthu ici; cifukwa cace, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.
22 Ndipo Yoabu anagwa nkhope yace pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yoabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yacita copempha mnyamata wace.
23 Comweco Yoabu ananyamuka namka ku Gesuri, nabwera naye Abisalomu ku Yerusalemu.
24 Ndipo mfumu inati, Apambukire ku nyumba yaiye yekha, koma asaone nkhope yanga. Comweco Abisalomu anapambukira ku nyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.
25 Ndipo m'lsrayeli monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri cifukwa ca kukongola kwace monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wace mwa iye munalibe cirema.
26 Ndipo pometa tsitsi lace amameta potsiriza caka, cifukwa tsitsi linamlemerera, cifukwa cace atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wace, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.
27 Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana amuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lace ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope.
28 Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu.
29 Pamenepo Abisalomu anaitana Yoabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yaciwiri, koma anakana kubwera.
30 Cifukwa cace iye anati kwa anyamata ace, Onani munda wa Yoabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.
31 Pamenepo Yoabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu ku nyumba yace, nanena naye, Cifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;
32 Abisalomu nayankha Yoabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kucokera ku Gesuri? mwenzi nditakhala komweko; cifukwa cace tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.
33 Comweco Yoabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yace pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.