2 Samueli 15 BL92

Kupanduka kwa Abisalomu, ndi kuthawa kwa Davide

1 Ndipo kunali, citapita ici Abisalomu anadzikonzera gareta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.

2 Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kucipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu ali yense ndi mrandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa ku mudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu; ndiye wa pfuko tina la Aisrayeli.

3 Abisalomu nanena naye, Ona zokamba zako ndizo zabwino ndi zolungama; koma mfumu sinauze wina kuti adzamve za iwe.

4 Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mrandu wace kapena cifukwa cace, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamcitira zacilungamo!

5 Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu ali yense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lace, namgwira, nampsompsona.

6 Abisalomu anacitira zotero Aisrayeli onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mrandu wao; comweco Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israyeli.

7 Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikacite cowinda canga ndinaciwindira Yehova.

8 Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri m'Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.

9 Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Comweco ananyamuka, nanka ku Hebroni.

10 Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israyeli, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.

11 Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.

12 Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofeli Mgiloni, mphungu wa Davide, ku mudzi wace ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo ciwembuco cinali colimba; pakuti anthu anacurukacurukabe kwa Abisalomu.

13 Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israyeli itsata Abisalomu.

14 Ndipo Davide ananena nao anyamata ace onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kucoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.

15 Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.

16 Mfumu nituruka, ndi banja lace lonse tinamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi ang'ono, kusunga nyumbayo.

17 Ndipo mfumu inaturuka, ndi anthu onse anamtsata; naima ku nyumba ya payokha.

18 Ndipo anyamata ace onse anapita naye limodzi; ndi Akereri ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kucokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.

19 Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopitikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.

20 Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? ubwerere nubwereretsenso abale ako; cifundo ndi zoonadi zikhale nawe.

21 Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.

22 Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ace onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye.

23 Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kucipululu.

Zadoki ndi Abyatara abwerera ndi likasa ku Yerusalemu

24 Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la cipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kuturuka m'mudzimo.

25 Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwererenalo likasa la Mulungu kumudziko; akandikomera mtima Yehova, iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso gi, ndi pokhala pace pomwe.

26 Koma iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andicitire cimene cimkomera.

27 Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Jonatani mwana wa Abyatara.

28 Ona ndidzaima pa madooko a m'cipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine.

29 Cifukwa cace Zadoki ndi Abyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.

30 Ndipo Davide anakwera pa cikweza ca ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anapfunda mutu wace nayenda ndi mapazi osabvala; ndi anthu onse amene anali naye anapfunda munthu yense mutu wace, ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.

31 Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofeli ali pakati pa opangana ciwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofeli ukhale wopusa.

32 Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai M-ariki anadzakomana naye ali ndi maraya ace ong'ambika, ndi dothi pamutu pace.

33 Ndipo Davide ananena naye, Ukapita pamodzi ndi ine udzandilemetsa;

34 koma ukabwerera kumudzi, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofeli.

35 Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abyatara ansembewo kodi? motero ciri conse udzacimva ca m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abyatara ansembewo.

36 Onani, ali nao komweko ana amuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Jonatani mwana wa Abyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze ciri conse mudzacimva.

37 Comweco Husai bwenzi la Davide anadza m'mudzimo; ndipo Abisalomu anafika ku Yerusalemu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24