2 Samueli 7 BL92

Mulungu salola Davide ammangire nyumba

1 Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwace, atampumulitsa Yehova pa adani ace onse omzungulira,

2 mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndirikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu liri m'kati mwa nsaru zocinga.

3 Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani mucite conse ciri mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu,

4 Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti,

5 Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?

6 pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinaturutsa ana a Israyeli ku Aigupto kufikira lero lomwe, kama ndinayenda m'cihema ndi m'nyumba wamba.

7 M'malo monse ndinayendamo limodzi ndi ana onse a Israyeli kodi ndinanena ndi pfuko limodzi la Aisrayeli, limene ndinalamulira kudyetsa anthu anga Aisrayeli, kuti, Munalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?

8 Cifukwa cace tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakucotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israyeli,

9 Ndipo ndinali nawe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akuru ali pa dziko lapansi,

10 Ndipo ndidzaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawabvutanso, monga poyamba paja,

11 monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israyeli; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

12 Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzaturuka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.

13 Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wace ku nthawi zonse.

14 Ndidzakhala atate wace, iye nadzakhala mwana wanga; akacita coipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;

15 koma cifundo canga sicidzamcokera iye, monga ndinacicotsera Sauli amene ndinamcotsa pamaso pako.

16 Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wacifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.

17 Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide.

18 Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhalapansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi ciani kuti munandifikitsa pano?

19 Ndipo icinso cinali pamaso panu cinthu cacing'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikuru irinkudza; ndipo mwatero monga mwa macitidwe a anthu, Yehova Mulungu!

20 Ndipo Davide adzaonjezanso kunenanso ndi Inuj pakuti mudziwa mnyamata wanu, Yehova Mulungu.

21 Cifukwa ca mau anu, ndi monga mwa mtima wanu, munacita ukuru wonse umene kuuzindikiritsa mnyamata wanu.

22 Cifukwa cace wamkuru ndi Inu Yehova. Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.

23 Ndiponso mtundu uti wa pa dziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israyeli, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ace, ndi kuti limveke dzina lace, ndi kukucitirani zinthu zazikuru ndi kucitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwaturutsa ku dziko la Aigupto mwa amitundu ndi milungu yao?

24 Ndipo mwadzikhazikira anthu anu Aisrayeli, akhale anthu anu nthawi zonse, ndipo Inu Yehova munakhala Mulungu wao.

25 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yace, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimucite monga munalankhula.

26 Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wit makamu ndiye Mulungu wa Israyeli, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu.

27 Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, munaulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; cifukwa cace mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero gi kwa Inu.

28 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munaloniezana ndi mnyamata wanu kumcitira cabwino ici,

29 cifukwa cace tsono cikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu cikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munacinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24