1 Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;
2 ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofoka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;
3 ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere.
4 Ndipo mauwa anamuyenerera Abisalomu, ndi akuru onse a Israyeli.
5 Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai M-ariki yemwe, timvenso cimene anene iye.
6 Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofeli analankhula mau akuti; ticite kodi monga mwa kunena kwace? ngati iai, unene ndiwe.
7 Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofeli suli wabwino.
8 Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ace kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga cimbalangondo cocilanda ana ace kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
9 Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, ali yense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.
10 Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wace ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisrayeli onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.
11 Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisrayeli onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mcenga uli panyanja kucuruka kwao; ndi kuti muturuke kunkhondo mwini wace.
12 Comweco tidambvumbulukira pa malo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye.
13 Ndiponso ngati walowa ku mudzi wina, Aisrayeli onse adzabwera ndi zingwe kumudziko, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang'ono kumeneko.
14 Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israyeli anati, Uphungu wa Husai M-ariki uposa uphungu wa Ahitofeli. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofeli kuti Yehova akamtengere Abisalomucoipa.
15 Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abyatara ansembewo, Ahitofeli anapangira Abisalomu ndi akuru a Israyeli zakuti zakuti; koma ine ndinapangira zakuti zakuti.
16 Cifukwa cace tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti, Musagona usiku uno pa madooko a kucipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.
17 Ndipo Jonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogeli; mdzakazi adafopita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mudzi.
18 Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anacoka msanga onse awiri, nafika ku nyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali naco citsime pabwalo pace; ndipo anatsikira m'menemo.
19 Ndipo mkazi anatenga cibvundikilo naciika pakamwa pa citsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sicinadziwika.
20 Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Jonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kumka ku Yerusalemu.
21 Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anaturuka m'citsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofeli anapangira zotere pa inu.
22 Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordano. Kutaca m'mawa sanasowa mmodzi wa iwo wosaoloka Yordano.
23 Ndipo Ahitofeli, pakuona kuti sautsata uphungu wace anamanga buru wace, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lace, nadzipacika, nafa, naikidwa m'manda a atate wace.
24 Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordano, iye ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye.
25 Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yoabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lace Itra M-israyeli, amene analowa kwa Abigayeli, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yoabu.
26 Ndipo Israyeli ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Gileadi.
27 Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyeli wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgileadi wa ku Rogelimu,
28 iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina,
29 ndi uci ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kutiadye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'cipululumo.