2 Samueli 12 BL92

Kulapa ndi kulangidwa kwa Davide

1 Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Pa mudzi wina panali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.

2 Wolemerayo anali nazo zoweta zazing'ono ndi zazikuru zambiri ndithu;

3 koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ace. Kanadyako cakudya cace ca iye yekha, kanamwera m'cikho ca iye yekha, kanagona pa cifukato cace, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wace wamkazi.

4 Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zace zazing'ono ndi zazikuru, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwana wa nkhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.

5 Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anacita ici, ayenera kumupha;

6 ndipo adzabwezera mwa mwana wa nkhosayo ena anai, cifukwa anacita ici osakhala naco cifundo.

7 Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israyeli, ndinakupulumutsa m'dzanja la Sauli;

8 ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa cifukato cako, ndinakupatsanso nyumba ya Israyeli ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakucepera ndikadakuonjezera zina zakuti zakuti.

9 Cifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kucita cimene ciri coipa pamaso pace? Unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wace akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.

10 Cifukwa cace tsono lupanga silidzacoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Mhiti akhale mkazi wako.

11 Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzacotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa liri denene.

12 Pakuti iwe unacicita m'tseri; koma Ine ndidzacita cinthu ici pamaso pa Aisrayeli onse, dzuwa liri nde.

13 Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinacimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wacotsa chimo lanu, simudzafa.

14 Koma popeza pakucita ici munapatsa cifukwa cacikuru kwa adani a Yehova ca kucitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.

15 Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri.

16 Cifukwa cace Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.

17 Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.

18 Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwang kuti mwana wafa; sadzadzicitira coipa nanga?

19 Koma pamene Davide anaona anyamata ace alikunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ace, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.

20 Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika ku nyumba yace; ndipo powauza anamuikira cakudya, nadya iye.

21 Pamenepo anyamata ace ananena naye, Ici mwacita nciani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya,

22 Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandicitira cifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.

23 Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.

Kubadwa kwa Solomo

24 Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wace, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Solomo. Ndipo Yehova anamkonda iye,

25 natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namucha dzina lace Wokondedwa ndi Yehova, cifukwa ca Yehova.

26 Ndipo Yoabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wacifumu.

27 Yoabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mudzi wa pamadzi.

28 Cifukwa cace tsono musonkhanitseanthu otsalawo, nimumangire mudziwo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mudziwo, ndipo ungachedwe ndi dzina langa.

29 Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda.

30 Nacotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwace kunali talente wa golidi; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye naturutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri.

31 Naturutsa anthu a m'mudzimo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi nkhwangwa zacitsulo; nawapsitiriza ndi citsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kumka ku Yerusalemu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24