2 Samueli 18 BL92

1 Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.

2 Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yoabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yoabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzaturuka limodzi ndi inu.

3 Koma anthuwo anati, Simudzaturuka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; cifukwa cace tsono nkwabwino kuti mutithandize kuturuka m'mudzi.

4 Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzacita cimene cikomera inu. Mfumu niima pambali pa cipata, ndipo anthu onse anaturuka ali mazana, ndi zikwi.

5 Ndipo mfumu inalamulira Yoabu nd Abisai ndi ltai, kuti, Cifukwa ca ine mucite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.

6 Comweco anthuwo anaturukira kuthengo kukamenyana ndi Israyeli; nalimbana ku nkhalango ya ku Efraimu.

7 Ndipo anthu a Israyeli anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukuru kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri.

8 Pakuti nkhondo inatanda pa dziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.

9 Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yace, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkuru. Ndipo mutu wace unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye Inapitirira.

10 Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yoabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.

11 Ndipo Yoabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? ndipo ine ndikadakupatsa ndarama khumi ndi lamba.

12 Munthuyo nanena ndi Yoabu, Ndingakhale ndikalandira ndarama cikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi ltai, kuti, Cenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.

13 Ndikadacita conyenga pa moyo wace, palibe mrandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsuta.

14 Pomwepo Yoabu anati, Sindiyenera kucedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.

15 Ndipo anyamata khumi onyamula zida zace za Yoabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha.

16 Ndipo Yoabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupitikitsa Aisrayeli; pakuti Yoahu analetsa anthuwo.

17 Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'cidzenje cacikuru kunkhalangoko; naunjika pamwamba pace mulu waukuru ndithu wamiyala; ndipo Aisrayeli onse anathawa yense ku hema wace.

18 Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira coimiritsaco ciri m'cigwa ca mfumu; pakuti anati, Ndiribe mwana wamwamuna adzakhala cikumbutso ca dzina langa; nacha coimiritsaco ndi dzina la iye yekha; ndipo cichedwa cikumbutso ca Abisalomu, kufikira lero lomwe.

Davide alira Abisalomu

19 Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera cilango adani ace.

20 Ndipo Yoabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, cifukwa mwana wa mfumu wafa.

21 Pamenepo Yoabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yoabu, nathamanga.

22 Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kaciwiri kwa Yoabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yoabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo?

23 Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange, iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kucigwa, napitirira Mkusi.

24 Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la cipata ca kulinga, natukula maso ace, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.

25 Pamenepo mlondayo anapfuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.

26 Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakucipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, iyenso abwera ndi mau.

27 Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki, Ndipo mfumu inati, iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.

28 Ndipo Ahimaazi anapfuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yace pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.

29 Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yoabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringu piringu, koma sindinadziwa ngati kutani.

30 Ndipo mfumu inati, Pambuka nuime apa. Napambuka, naimapo.

31 Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera cilango lero onse akuukira inu.

32 Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukucitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.

33 Ndipo mfumuyo inagwidwa cisoni, nikwera ko cipinda cosanja pa cipataco, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24