2 Samueli 6 BL92

Atenga likasa la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu

1 Pambuyo pace Davide anamemezanso osankhika onse a m'Israyeli, anthu zikwi makumiatatu.

2 Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nacokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amachula nalo Dzinalo Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.

3 Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa gareta watsopano, ataliturutsa m'nyumba ya Abinadabu, iri pacitunda, ndipo Uza ndi Ahio ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa gareta watsopanoyo.

4 Poturuka nalo tsono pamodzi ndi likasa la Mulungu m'nyumba ya Abinadabu iri pacitunda, Ahio anatsogolera likasalo.

5 Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoyimbira za mitundu mitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi masece, ndi nsanje.

6 Ndipo pofika iwo ku dwale la Nakoni, Uza anatambasula dzanja lace, nacirikiza likasa la Mulungu; cifukwa ng'ombe zikadapulumuka.

7 Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, cifukwa ca kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.

8 Ndipo kudaipira Davide, cifukwa Yehova anacita cipasulo ndi Uza; nacha-malowo Cipasulo ca Uza, kufikira lero lino.

9 Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?

10 Momwemo Davide sanafuna kudzitengera likasa la Yehova lidze ku mudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.

11 Ndipo a likasa la Yehova linakhala m'nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa Obedi-Edomu ndi banja lace lonse.

Akwera nalo likasalo kuleka ku Yerusalemu

12 Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obedi-Edomu ndi zace zonse, cifukwa ca likasa la Mulungu. Comweco Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu, nakwera nalo ku mudzi wa Davide, ali ndi cimwemwe.

13 Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi conenepa cina.

14 Ndipo Davide anabvina ndi mphamvu yace yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.

15 Comweco Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anakwera nalo likasa la Yehova, ndi cimwemwe ndi kulira kwa malipenga,

16 Ndipo kunali pamene likasa la Yehova tinafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikubvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwace.

17 Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analgka pamalo pace pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.

18 Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu.

19 Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israyeli, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa, Ndipo anthu aja onse anabwera yense ku nyumba yace.

20 Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yace. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli anaturukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israyeli inalemekezeka ndithu, amene anabvula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ace, monga munthu woluluka abvula wopanda manyazi!

21 Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lace lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israyeli, cifukwa cace ndidzasewera pamaso pa Yehova.

22 Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzicepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.

23 Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli sanaona mwana kufikira tsiku la imfa yace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24