2 Samueli 23 BL92

Nyimbo yotsiriza ya Davide

1 Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:—Atero Davide mwana wa Jese,Atero munthu wokwezedwa,Ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,Ndi mwini masalmo wokoma wa Israyeli:

2 Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,Ndi mau ace anali pa lilime langa,

3 Mulungu wa Israyeli anati,Thanthwe la Israyeli Gnalankhula ndi ine;Kudzakhala woweruza anthu molungama;Woweruza m'kuopa Mulungu.

4 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, poturuka dzuwa,M'mawa mopanda mitambo;Pamene msipu uphuka kuturuka pansi,Cifukwa ca kuwala koyera, italeka mvula.

5 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu;Koma iye anapangana ndi ine pangano losatha,Lolongosoka mwa zonse ndi losungika;Pakuti ici ndi cipulumutso canga conse, ndi kufuma kwanga konse,Kodi sadzacimeretsa?

6 Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,Pakuti siigwiridwa ndi dzanja;

7 Koma wakukhudza iyo adzikonzeratu citsulo ndi luti la mkondo;Ndipo idzatenthedwa konse ndi mota m'malo mwao.

Angwazi a Davide

8 Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Josebu-basebete Mtakemoni, mkuru wa akazembe; ameneyu ndiye Adino M-ezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.

9 Ndipo wotsatana naye Eleazeri mwana wa Dodai mwana wa M-akohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atacoka Aisrayeli;

10 iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lace linalema, ndi dzanja lace lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwace kukafunkha kokha.

11 Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Mharario Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12 Koma iyeyoanaima pakati pa mundawo, naucinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru.

13 Ndipo atatu a mwamakumi atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti Gnamanga zithando m'cigwa ca Refaimu.

14 Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali m'Betelehemu.

15 Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! wina akadandipatsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri pacipatapo!

16 Ndipongwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'citsime ca ku Betelehemu, ca pa cipataco, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafuna kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.

17 Nati, Ndisacite ici ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa ana pitawa ndi kutaya moyo wao? Cifukwa cace iye anakana kumwa. Izi anazicita ngwazi zitatuzi.

18 Ndipo Abisai, mbale wa Yoabu, mwana wa Zeruya, anali wamkuru wa atatuwa. Iye natukula mkondo wace pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19 Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? cifukwa cace anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba.

20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabzeli amene anacita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Moabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya cipale cofewa;

21 ndipo anapha M-aigupto munthu wokongola, M-aigupto anali nao mkondo m'dzanja lace; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22 Izi anacita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23 Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ace.

24 Asaheli mbale wa Yoabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;

25 Sama Mharodi, Elika Mharodi;

26 Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekoi.

27 Abiyezeri M-anetori, Mebunai Mhusati;

28 Zalimoni M-ahohi, Maharai Mnefati;

29 Helebi mwana wa Baana Mnetofati, ltai mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa ana a Benjamini;

30 Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi;

31 Abialiboni M-aribati, Azmaveti Mbahurimi;

32 Eliaba Mshaliboni wa ana a Jaseni, Jonatani;

33 Sama Mharari, Ahiamu mwana wa Sarari Mharari;

34 Elifaleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaacha, Eliamu mwana wa Ahitofeli Mgiloni;

35 Hezra wa ku Karimeli, Paarai M-aribi;

36 Igali mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi;

37 Zeleki M-amoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yoabu mwana wa Zeruya;

38 Ira M-itri, Garebi M-itri;

39 Uriya Mhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24