9 Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Comweco ananyamuka, nanka ku Hebroni.
10 Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israyeli, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.
11 Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.
12 Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofeli Mgiloni, mphungu wa Davide, ku mudzi wace ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo ciwembuco cinali colimba; pakuti anthu anacurukacurukabe kwa Abisalomu.
13 Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israyeli itsata Abisalomu.
14 Ndipo Davide ananena nao anyamata ace onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kucoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.
15 Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.