17 Ndipo anali nao anthu cikwi cimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saul; ndi ana ace amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ace makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordano pamaso pa mfumu.
18 Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kucita comkomera. Ndipo Simeyi mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordano.
19 Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukile cimene mnyamata wanu ndinacita mwamphulupulu tsiku lila mbuye wanga mfumu anaturuka ku Yerusalemu, ngakhale kucisunga mumtima mfumu.
20 Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinacimwa; cifukwa cace, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.
21 Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simeyi cifukwa ca kutemberera wodzozedwa wa Yehova?
22 Koma Davide anati, Ndiri ndi ciani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israyeli lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israyeli lero?
23 Ndipo mfumu inanena ndi Simeyi, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye.