1 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mudzi wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.
2 Comweco Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ace awiri, ndiwo Ahingamu Mjezreeli, ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.
3 Ndipo Davide anakwera nao anyamata ace okhala naye, munthu yense ndi banja lace; iwowa nakhala m'midzi ya Hebroni.
4 Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda.Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Jabezi Gileadi ndiwo amene anamuika Sauli.