29 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;Ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;Ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31 Kunena za Mulungu, njira yace iri yangwiro;Mau a Yehova anayesedwa; iye ndiye cikopa kwa onse akukhulupirira iye.
32 Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33 Mulungu ndiye Gnga langa lamphamvu;Ndipo iye ayendetsa angwiro mu njira yace.
34 Iye asandutsa mapazi ace akunga mapazi a mbawala;Nandiika pa misanje yanga.
35 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.