36 Ndiponso munandipatsa cikopa ca cipulumutso canu;Ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,Ndi mapazi anga sanaterereka.
38 Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga;Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.
39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,Inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40 Pakuti Inu munandimanga m'cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.
41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42 Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.