41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42 Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.
43 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati pfumbi la padziko,Ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.
44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.
45 Alendo adzandigonjera ine,Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.
46 Alendo adzafota,Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.
47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;