44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.
45 Alendo adzandigonjera ine,Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.
46 Alendo adzafota,Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.
47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;
48 Inde Mulungu wakundibwezera cilango ine,Ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.
49 Amene anditurutsa kwa adani anga;Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.
50 Cifukwa cace ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,Ndipo ndidzayimba zolemekeza dzina lanu.